MASALIMO19nya_bib
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide.
1Zakumwamba zimalengeza za ulemerero wa Mulungu;thambo limalalikira ntchito za manja ake.2Tsiku ndi tsiku zimayankhula mawu ambiri,usiku ndi usiku zimaonetsa poyera nzeru.3Palibe kuyankhula, palibe mawu aliwonse;liwu lawo silimveka.4Koma uthenga wawo umapita pa dziko lonse lapansi,mawuwo amafika mpakakumalekezero a dziko lapansi.5Dzuwa lili ngati mkwatibwi wobwera kuchokera ku nsanja yake,ngati katswiri wokondwerera kuthamanga pa mpikisano.6Limatuluka kuyambira mbali ina ya thambondi kuzungulira mpaka mbali inanso;palibe chinthu chotha kupewa kutentha kwake.7Lamulo la Yehova ndi langwiro,kutsitsimutsa moyo.Maumboni a Yehova ndi odalirika,amapereka nzeru kwa wopanda nzeru.8Malangizo a Yehova ndi olungama,amapereka chimwemwe mu mtima.Malamulo a Yehova ndi onyezimira,amapereka kuwala.9Kuopa Yehova ndiye chinthu changwiro,chimakhala mpaka muyaya.Maweruzo a Yehova ndi owonandipo onse ndi olungama;10ndi a mtengowapatali kuposa golide,kuposa golide weniweni;ndi otsekemera kuposa uchi,kuposa uchi wochokera pa chisa chake.11Mtumiki wanu amachenjezedwa nawo;powasunga pali mphotho yayikulu.12Ndani angathe kudziwa zolakwa zake?Mundikhululukire zolakwa zanga zobisika.13Muteteze mtumiki wanunso ku machimo ochita akudziwa;iwo asandilamulire.Kotero ndidzakhala wosalakwa,wopanda mlandu wa tchimo lalikulu.14Mawu a mʼkamwa mwanga ndi zolingalira za mu mtima mwangazikhale zokondweretsa pamaso panu,Inu Yehova, Thanthwe langa ndi Mpulumutsi wanga.