MASALIMO149nya_bib

1Tamandani Yehova.Imbirani Yehova nyimbo yatsopano,matamando ake mu msonkhano wa oyera mtima.
2Israeli asangalale mwa mlengi wake;anthu a ku Ziyoni akondwere mwa Mfumu yawo.3Atamande dzina lake povinandi kuyimbira Iye nyimbo ndi tambolini ndi pangwe.4Pakuti Yehova amakondwera ndi anthu ake;Iye amaveka chipulumutso odzichepetsa.5Oyera mtima asangalale mu ulemu wakendi kuyimba mwachimwemwe pa mabedi awo.
6Matamando a Mulungu akhale pakamwa pawo,ndi lupanga lakuthwa konsekonse mʼmanja mwawo,7kubwezera chilango anthu a mitundu ina,ndi kulanga anthu a mitundu yonse,8kumanga mafumu awo ndi zingwe,anthu awo otchuka ndi unyolo wachitsulo,9kuchita zimene zinalembedwa zotsutsana nawoUwu ndi ulemerero wa oyera mtima ake onse.Tamandani Yehova.