MASALIMO142nya_bib
Ndakatulo ya Davide, pamene iyeyo anali mʼphanga. Pemphero.
1Ndikulirira Yehova mofuwula;ndikukweza mawu anga kwa Yehova kupempha chifundo.2Ndikukhuthula madandawulo anga pamaso pake;ndikufotokoza za masautso anga pamaso pake.3Pamene mzimu wanga walefuka mʼkati mwanga,ndinu amene mudziwa njira yanga.Mʼnjira imene ndimayendamoanthu anditchera msampha mobisa.4Yangʼanani kumanja kwanga ndipo onani;palibe amene akukhudzika nane.Ndilibe pothawira;palibe amene amasamala za moyo wanga.5Ndilirira Inu Yehova;ndikuti, “Ndinu pothawirapo panga,gawo langa mʼdziko la anthu amoyo.”6Mverani kulira kwangapakuti ndathedwa nzeru;pulumutseni kwa amene akundithamangitsapakuti ndi amphamvu kuposa ine.7Tulutseni mʼndende yangakuti nditamande dzina lanu.Ndipo anthu olungama adzandizungulirachifukwa cha zabwino zanu pa ine.No translations available.