MASALIMO137nya_bib

1Mʼmbali mwa mitsinje ya ku Babuloni tinakhala pansi ndi kulirapamene tinakumbukira Ziyoni.2Kumeneko, pa mitengo ya misondozitinapachika apangwe athu,3pakuti anthu otigwira ukapolo anatipempha kuti tiyimbe nyimbo.Otizunza athu anafuna nyimbo zachisangalalo;iwo anati, “Tiyimbireni imodzi mwa nyimbo za ku Ziyoni!”
4Tingayimbe bwanji nyimbo za Yehovamʼdziko lachilendo?5Ndikakuyiwala iwe Yerusalemu,dzanja langa lamanja liyiwale luso lake.6Lilime langa limamatire ku nkhama za mʼkamwa mwangandikapanda kukukumbukira iwe Yerusalemu,ngati sindiyesa iwechimwemwe changa chachikulu.
7Kumbukirani, Inu Yehova, zimene Aedomu anachitapa tsiku limene Yerusalemu anagonja.Iwowo anafuwula kuti, “Mugwetseni pansi, mugwetseni pansimpaka pa maziko ake!”
8Iwe mwana wa mkazi wa Babuloni, woyenera kuwonongedwa,wodalitsika ndi yemwe adzakubwezerapa zimene watichitira.9Amene adzagwira makanda akondi kuwakankhanthitsa pa miyala.