MASALIMO129nya_bib
Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu.
1“Andizunza kwambiri kuyambira ubwana wanga,”anene tsono Israeli;2“Andizunza kwambiri kuyambira ubwana wanga,koma sanandipambane.3Anthu otipula analima pa msana pangandipo anapangapo mizere yayitali:4Koma Yehova ndi wolungama;Iye wandimasula ku zingwe za anthu oyipa.”5Onse amene amadana ndi Ziyoniabwezedwe pambuyo mwamanyazi.6Akhale ngati udzu womera pa denga la nyumba,umene umafota usanakule;7sungadzaze manja a owumwetakapena manja a omanga mitolo.8Odutsa pafupi asanene kuti,“Dalitso la Yehova lili pa inu;tikukudalitsani mʼdzina la Yehova.”