MASALIMO127nya_bib

Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu. Salimo la Solomoni.

1Yehova akapanda kumanga nyumba,omanga nyumbayo agwira ntchito pachabe.Yehova akapanda kulondera mzinda,mlonda akanangolondera pachabe.2Mumangodzivuta nʼkulawirira mmamawandi kusagona msanga madzulo,kuvutikira chakudya choti mudye,pakuti Iye amapereka tulo kwa amene amawakonda.
3Ana ndiye cholowa chochokera kwa Yehova,ana ndi mphotho yochokera kwa Iye.4Ana a pa unyamata ali ngati mivi mʼmanjamwa munthu wankhondo.5Wodala munthuamene motengera mivi mwake mwadzaza.Iwo sadzachititsidwa manyazipamene alimbana ndi adani awo pa zipata.