MASALIMO124nya_bib
Salimo la Davide. Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu.
1Akanapanda kukhala mbali yathu Yehova,anene tsono Israeli,2akanapanda kukhala mbali yathu Yehova,potiwukira anthuwo,3iwo atatipsera mtima,akanatimeza amoyo;4chigumula chikanatimiza,mtsinje ukanatikokolola,5madzi a mkokomoakanatikokolola.6Atamandike Yehova,amene sanalole kuti tikhale chakudya cha mano awo.7Moyo wathu wawonjoka ngati mbalameyokodwa mu msampha wa mlenje;msampha wathyoka,ndipo ife tapulumuka.8Thandizo lathu lili mʼdzina la Yehovawolenga kumwamba ndi dziko lapansi.