MASALIMO121nya_bib

Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu.

1Ndikweza maso anga ku mapiri;kodi thandizo langa limachokera kuti?2Thandizo langa limachokera kwa Yehova,wolenga kumwamba ndi dziko lapansi.
3Sadzalola kuti phazi lako literereke;Iye amene amakusunga sadzawodzera.4Taonani, Iye amene amasunga Israelisadzawodzera kapena kugona.
5Yehova ndiye amene amakusunga;Yehova ndiye mthunzi wako ku dzanja lako lamanja.6Dzuwa silidzakupweteka nthawi ya masana,kapena mwezi nthawi ya usiku.
7Yehova adzakuteteza ku zoyipa zonse;adzasunga moyo wako.8Yehova adzayangʼanira kutuluka kwako ndi kulowa kwako;kuyambira tsopano mpaka muyaya.