MASALIMO12nya_bib

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Monga mwa mayimbidwe seminiti. Salimo la Davide.

1Thandizeni Yehova pakuti palibe munthu wokhulupirika;okhulupirika akusowa pakati pa anthu.2Aliyense amanamiza mʼbale wake;ndi pakamwa pawo pabodza amayankhula zachinyengo.
3Inu Yehova tsekani milomo yonse yachinyengondi pakamwa paliponse podzikuza.4Pakamwa pamene pamati, “Ife tidzapambana ndi kuyankhula kwathu;pakamwapa ndi pathupathu, tsono mbuye wathu ndani?”
5“Chifukwa cha kuponderezedwa kwa anthu opanda mphamvundi kubuwula kwa anthu osowa,Ine ndidzauka tsopano,” akutero Yehova,“Ndidzawateteza kwa owazunza.”6Ndipo mawu a Yehova ndi angwiromonga siliva oyengedwa mʼngʼanjo yadothi,oyengedwa kasanu nʼkawiri.
7Inu Yehova mudzatitchinjiriza ndipomudzatiteteza kwa anthu otere kwamuyaya.8Oyipa amangoyendayenda ponseponseanthu akamayamikira zochita zawo.