MASALIMO117nya_bib

1Tamandani Yehova, inu anthu a mitundu yonse;mulemekezeni Iye, inu mitundu ya anthu.2Pakuti chikondi chake pa ife ndi chachikulu,ndipo kukhulupirika kwa Yehova nʼkosatha.Tamandani Yehova.