MASALIMO115nya_bib

1Kwa ife ayi Yehova, kwa ife ayikoma ulemerero ukhale pa dzina lanu,chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika ndiponso chifukwa cha kukhulupirika kwanu.
2Chifukwa chiyani anthu a mitundu ina akunena kuti,“Mulungu wawo ali kuti?”3Mulungu wathu ali kumwamba;Iye amachita chilichonse chimene chimamukondweretsa.4Koma mafano awo ndi siliva ndi golide,opangidwa ndi manja a anthu.5Pakamwa ali napo koma sayankhula,maso ali nawo koma sapenya;6makutu ali nawo koma samva,mphuno ali nazo koma sanunkhiza;7manja ali nawo koma akakhudza samva kanthu;mapazi ali nawo koma sayenda;kapena pakhosi pawo kutulutsa mawu.8Anthu amene amapanga mafanowo adzafanana nawo,chimodzimodzinso onse amene amadalira mafanowo.
9Inu Aisraeli, dalirani Yehova;Iye ndiye thandizo lanu ndi chishango chanu.10Iwe nyumba ya Aaroni, dalira Yehova;Iye ndiye thandizo lako ndi chishango chako.11Inu amene mumaopa Iye, dalirani Yehova;Iye ndiye thandizo lanu ndi chishango chanu.
12Yehova watikumbukira ndipo adzatidalitsa:adzadalitsa nyumba ya Israeli,adzadalitsa nyumba ya Aaroni,13adzadalitsa iwo amene amaopa Yehova;aangʼono ndi aakulu omwe.
14Yehova akuwonjezereni madalitso;inuyo pamodzi ndi ana anu.15Mudalitsidwe ndi Yehova,Wolenga kumwamba ndi dziko lapansi.
16Kumwamba ndi kwa Yehova,koma dziko lapansi Iye walipereka kwa anthu.17Si anthu akufa amene amatamanda Yehova,amene amatsikira kuli chete;18ndi ife amene timatamanda Yehova,kuyambira tsopano mpaka muyaya.Tamandani Yehova.