MASALIMO112nya_bib
1Tamandani Yehova.Wodala munthu amene amaopa Yehova,amene amakondwera kwambiri ndi malamulo ake.2Ana ake adzakhala amphamvu mʼdziko;mʼbado wa olungama mtima udzadalitsidwa.3Kulemera ndi chuma zili mʼnyumba yake,ndipo chilungamo chake ndi chosatha.4Ngakhale mu mdima kuwala kumatulukira olungama mtima;wokoma mtima, wachifundo ndi wowongoka mtima.5Zinthu zabwino zidzabwera kwa iye amene amapereka mowolowamanja ndi wokongoletsa mwaufulu,amene amachita ntchito yake mwachilungamo.6Ndithu sadzagwedezeka;munthu wolungama sadzayiwalika mpaka muyaya.7Saopa akamva zoyipa zimene zachitika;mtima wake ndi wokhazikika ndipo amadalira Yehova.8Mtima wake ndi wotetezedwa, sadzakhala ndi mantha;potsiriza pake adzayangʼana adani ake mwachipambano.9Wopereka mphatso zake mowolowamanja kwa osauka,chilungamo chake chimanka mpaka muyaya;nyanga yake idzakwezedwa mwaulemu.10Munthu woyipa adzaona zimenezi ndipo adzapsa mtima;adzakukuta mano ake ndipo adzasungunuka.Zolakalaka za anthu oyipa sizidzachitika konse.