MASALIMO110nya_bib

Salimo la Davide.

1Yehova akuwuza Mbuye wanga kuti,“Khala ku dzanja langa lamanjampaka nditasandutsa adani akokukhala chopondapo mapazi ako.”
2Yehova adzakuza ndodo yamphamvu ya ufumu wako kuchokera mʼZiyoni;udzalamulira pakati pa adani ako.3Ankhondo ako adzakhala odziperekapa tsiku lako la nkhondo.Atavala chiyero chaulemerero,kuchokera mʼmimba ya mʼbandakucha,udzalandira mame a unyamata wako.
4Yehova walumbirandipo sadzasintha maganizo ake:“Ndiwe wansembe mpaka muyayamonga mwa unsembe wa Melikizedeki.”
5Ambuye ali kudzanja lako lamanja;Iye adzaponda mafumu pa tsiku la ukali wake.6Adzaweruza anthu a mitundu ina,adzadzaza dziko lapansi ndi mitembo ndipo adzaphwanya olamulira a pa dziko lonse lapansi.7Iye adzamwa mu mtsinje wa mʼmbali mwa njira;choncho adzaweramutsa mutu wake.