MASALIMO107nya_bib

1Yamikani Yehova chifukwa ndi wabwino;pakuti chikondi chake ndi chosatha.2Owomboledwa a Yehova anene zimeneziamene Iyeyo anawawombola mʼdzanja la mdani,3iwo amene anawasonkhanitsa kuchokera ku mayiko,kuchokera kumadzulo ndi kummawa, kuchokera kumpoto ndi kummwera.
4Ena anayendayenda mʼchipululu mopanda kanthu,osapeza njira yopitira ku mzinda kumene akanakakhazikikako.5Iwo anamva njala ndi ludzu,ndipo miyoyo yawo inafowokeratu.6Pamenepo analirira Yehova mʼmavuto awondipo Iye anawapulumutsa ku masautso awo.7Iye anawatsogolera mʼnjira yowongokakupita ku mzinda umene anakakhazikikako.8Ayamike Yehova chifukwa cha chikondi chake chosathandi chifukwa cha machitidwe ake odabwitsa kwa anthu onse,9pakuti Iye wapha ludzu la munthu womva ludzundipo wakhutitsa wanjala ndi zinthu zabwino.
10Ena anakhala mu mdima ndi mʼchisoni chachikulu,amʼndende ovutika mʼmaunyolo achitsulo,11pakuti iwowo anawukira mawu a Mulungundi kunyoza uphungu wa Wammwambamwamba.12Kotero Iye anawapereka kuti agwire ntchito yakalavulagaga;anagwa pansi ndipo panalibe woti awathandize.13Pamenepo analirira Yehova mʼmasautso awondipo Iye anawapulumutsa ku masautso awo.14Yehova anawatulutsa mu mdima ndi mʼchisoni chachikulundipo anadula maunyolo awo.15Ayamike Yehova chifukwa cha chikondi chake chosathandi machitidwe ake odabwitsa kwa anthu onse,16pakuti Iye amathyola zipata zamkuwandi kudula pakati mipiringidzo yachitsulo.
17Ena anakhala zitsiru chifukwa cha njira zawo zowukira,ndipo anamva zowawa chifukwa cha mphulupulu zawo.18Iwo ananyansidwa ndi chakudya chilichonsendipo anafika pafupi ndi zipata za imfa.19Pamenepo analirira Yehova mʼmasautso awondipo Iye anawapulumutsa ku masautso awowo.20Iye anatumiza mawu ake ndi kuwachiritsa;anawalanditsa ku manda.21Ayamike Yehova chifukwa cha chikondi chake chosathandi machitidwe ake odabwitsa kwa anthu.22Apereke nsembe yachiyamikondi kufotokoza za ntchito zake ndi nyimbo zachimwemwe.
23Ena anayenda pa nyanja mʼsitima zapamadzi;Iwo anali anthu amalonda pa nyanja yayikulu.24Anaona ntchito za Yehova,machitidwe ake odabwitsa mʼnyanja yakuya.25Pakuti Iye anayankhula ndi kuwutsa mphepo yamkunthoimene inabweretsa mafunde ataliatali.26Sitima za pamadzizo zinatukulidwa mmwamba ndi kutsikira pansi pakuya;pamene amawonongeka, kulimba mtima kwawo kunasungunuka.27Anachita chizungulire ndi kudzandira ngati anthu oledzera;anali pa mapeto a moyo wawo.28Pamenepo analirira Yehova mʼmasautso awondipo Iyeyo anawapulumutsa ku masautso awo.29Yehova analetsa namondwe,mafunde a mʼnyanja anatontholetsedwa.30Anali osangalala pamene kunakhala bata,ndipo Iye anawatsogolera ku dooko limene amalifuna.31Ayamike Yehova chifukwa cha chikondi chake chosathandi machitidwe ake odabwitsa kwa anthu.32Akuze Iye mu msonkhano wa anthundi kumutamanda pabwalo la akuluakulu.
33Iye anasandutsa mitsinje kukhala chipululu,akasupe otuluka madzi kukhala nthaka yowuma,34ndiponso nthaka yachonde kukhala nthaka yamchere,chifukwa cha kuyipa kwa amene amakhala kumeneko.35Anasandutsa chipululu kukhala mayiwe a madzindi nthaka yowuma kukhala akasupe a madzi oyenda;36kumeneko Iye anabweretsa anthu anjala kuti azikhalako,ndipo iwo anamanga mzinda woti akhazikikeko.37Anafesa mbewu mʼminda ndi kudzala mipesandipo anakolola zipatso zochuluka;38Yehova anawadalitsa, ndipo chiwerengero chawo chinachuluka kwambiri,ndipo Iye sanalole kuti ziweto zawo zithe.
39Kenaka chiwerengero chawo chinachepa ndipo iwo anatsitsidwachifukwa cha mazunzo, mavuto ndi chisoni;40Iye amene amakhuthulira mʼnyozo pa olemekezekaanawachititsa kuyendayenda mʼmalo owumawo wopanda njira.41Koma Iyeyo anakweza anthu osowa kuchoka ku masautso awongati magulu a nkhosa.42Anthu olungama mtima amaona ndi kusangalala,koma anthu onse oyipa amatseka pakamwa pawo.
43Aliyense wanzeru asamalitse zinthu zimenezindi kuganizira za chikondi chachikulu cha Yehova.