MASALIMO101nya_bib
Salimo la Davide.
1Ndidzayimba za chikondi ndi chiweruzo chanu cholungama;kwa Inu Yehova ndidzayimba matamando.2Ndidzatsata njira yolungama;nanga mudzabwera liti kwa ine?Ndidzayenda mʼnyumba mwangandi mtima wosalakwa.3Sindidzayika chinthu chilichonse choyipapamaso panga.Ine ndimadana ndi zochita za anthu opanda chikhulupiriro;iwo sadzadziphatika kwa ine.4Anthu a mtima wokhota adzakhala kutali ndi ine;ine sindidzalola choyipa chilichonse kulowa mwa ine.5Aliyense wosinjirira mnansi wake mseriameneyo ndidzamuletsa;aliyense amene ali ndi maso amwano ndi mtima wodzikuza,ameneyo sindidzamulekerera.6Maso anga adzakhala pa okhulupirika mʼdziko,kuti akhale pamodzi ndi ine;iye amene mayendedwe ake ndi wosalakwaadzanditumikira.7Aliyense wochita chinyengosadzakhala mʼnyumba mwanga.Aliyense woyankhula mwachinyengosadzayima pamaso panga.8Mmawa uliwonse ndidzatontholetsa anthuonse oyipa mʼdziko;ndidzachotsa aliyense wochita zoyipamu mzinda wa Yehova.