MASALIMO100nya_bib

Salimo. Nyimbo yothokoza.

1Fuwulani kwa Yehova mwachimwemwe, inu dziko lonse lapansi.2Mulambireni Yehova mosangalala;bwerani pamaso pake ndi nyimbo zachikondwerero.3Dziwani kuti Yehova ndi Mulungu.Iye ndiye amene anatipanga ndipo ife ndife ake;ndife anthu ake, nkhosa za pabusa pake.
4Lowani ku zipata zake ndi chiyamikondi ku mabwalo ake ndi matamando;muyamikeni ndi kutamanda dzina lake.5Pakuti Yehova ndi wabwino ndipo chikondi chake ndi chamuyaya;kukhulupirika kwake nʼkokhazikika pa mibado ndi mibado.