MIYAMBO22nya_bib
1Mbiri yabwino ndi yofunika kuposa chuma chambiri;kupeza kuyanja nʼkwabwino kuposa siliva kapena golide.2Wolemera ndi wosauka ndi ofanana;onsewa anawalenga ndi Yehova.3Munthu wochenjera akaona choopsa amabisala,koma munthu wopusa amangopitirira ndipo amadzanongʼoneza bondo.4Mphotho ya munthu wodzichepetsandi woopa Yehova ndi chuma, ulemu ndi moyo.5Mʼnjira za anthu oyipa muli minga ndi misampha,koma amene amasala moyo wake adzazipewa zonsezo.6Mwana muzimuphunzitsa njira yake,ndipo akadzakalamba sadzachokamo.7Wolemera amalamulira wosauka,ndipo wokongola zinthu amakhala kapolo wa womukongozayo.8Amene amafesa zoyipa amakolola mavuto,ndipo ndodo yaukali wake idzathyoka.9Amene ali ndi diso lachifundo adzadalitsika,pakuti iye amagawana chakudya chake ndi anthu osauka.10Chotsani munthu wonyoza, ndipo kukangana kudzatha;mapokoso ndi zonyoza zidzaleka.11Amene amakonda kukhala woyera mtima ndi kumayankhula mawu abwino,adzakhala bwenzi la mfumu.12Maso a Yehova amakhala pa anthu odziwa bwino zinthu,koma Iye adzalepheretsa mawu a anthu osakhulupirika.13Munthu waulesi amati,“Kunjaku kuli mkango. Ine ndidzaphedwa mʼmisewu!”14Pakamwa pa mkazi wachigololo pali ngati dzenje lozama;amene Yehova wamukwiyira adzagwamo.15Uchitsiru umakhala mu mtima mwa mwana,koma ndodo yomulangira mwanayo idzachotsa uchitsiruwo.16Amene amapondereza anthu osauka kuti awonjezere chuma chake,ndiponso amene amapereka mphatso kwa anthu olemera onsewa adzasauka.