NAHUMU2nya_bib

Kugwa kwa Ninive

1Wodzathira nkhondo akubwerakudzalimbana nawe, Ninive.Tetezani malinga anu,dziyangʼanani ku msewu,konzekerani nkhondo,valani dzilimbe.2Yehova adzabwezeretsa ulemerero wa Yakobongati ulemerero wa Israeli,ngakhale anthu owononga anawawononga kotheratundipo anawononganso mpesa wawo.
3Zishango za ankhondo ake ndi zofiira;asilikali ake avala zovala zofiirira.Zitsulo za pa magaleta zikunyezimiratsiku la kukonzekera kwake.Akuonetsa mikondo ya mkungudza yonoledwa.4Magaleta akuthamanga mʼmisewuakungothamangathamanga pa mabwalo.Akuoneka ngati miyuni yoyaka;akuthamanga ngati chingʼaningʼani.
5Iye akuyitanitsa asilikali ake wolemekezeka,koma iwo akubwera napunthwa.Akuthamangira ku linga la mzinda;akuyimika chodzitchinjirizira pamalo pake.6Atsekula zipata zotchinga madzi a mu mtsinjendipo nyumba yaufumu yagwa.7Zatsimikizika kuti mzindautengedwa ndi kupita ku ukapolo.Akapolo aakazi akulira ngati nkhundandipo akudziguguda pachifuwa.8Ninive ali ngati dziwe,ndipo madzi ake akutayika.Iwo akufuwula kuti, “Imani! Imani!”Koma palibe amene akubwerera.9Funkhani siliva!Funkhani golide!Katundu wake ndi wochuluka kwambiri,chuma chochokera pa zinthu zake zamtengowapatali!10Iye wawonongedwa, wafunkhidwa ndipo wavulidwa!Mitima yasweka, mawondo akuwombana,anthu akunjenjemera ndiponkhope zasandulika ndi mantha.
11Kodi tsopano dzenje la mikango lili kuti,malo amene mikango inkadyetserako ana ake,kumene mkango waumuna ndi waukazi unkapitako,ndipo ana a mkango sankaopa kanthu kalikonse?12Mkango waumuna unkapha nyama yokwanira ana akendiponso kuphera nyama mkango waukazi,kudzaza phanga lake ndi zimene waphandiponso dzenje lake ndi nyama imene waphayo.
13Yehova Wamphamvuzonse akuti,“Ine ndikutsutsana nawe.Ndidzatentha magaleta ako mpaka utsi tolotolo,ndipo lupanga lidzapha mikango yako yayingʼono;sindidzakusiyira chilichonse choti udye pa dziko lapansi.Mawu a amithenga anu sadzamvekanso.”