MIKA1nya_bib
1Yehova anayankhula ndi Mika wa ku Moreseti pa nthawi ya ulamuliro wa Yotamu, Ahazi ndi Hezekiya, mafumu a ku Yuda. Awa ndi masomphenya amene iye anaona onena za Samariya ndi Yerusalemu.2Tamverani, inu anthu a mitundu yonse,mvetsera iwe dziko lapansi ndi okhala mʼmenemo,pakuti Ambuye Yehova achitira umboni wokutsutsani,Ambuye akuyankhula ali mʼnyumba yake yopatulika.