MALIRO4nya_bib
1Haa! Golide wathimbirira,golide wosalala wasinthikiratu!Amwazamwaza miyala yokongola ya kumalo opatulikapamphambano ponse pa mzinda.2Haa! Ana a Ziyoni amtengowapataliamene kale anali ngati golide,tsopano ali ngati miphika ya dothi,ntchito ya owumba mbiya!3Ngakhale nkhandwe zimapereka berekuyamwitsa ana ake,koma anthu anga asanduka ankhanzangati nthiwatiwa mʼchipululu.4Lilime la mwana lakangamira kukhosichifukwa cha ludzu,ana akupempha chakudya,koma palibe amene akuwapatsa.5Iwo amene kale ankadya zononaakupemphetsa mʼmisewu ya mu mzinda.Iwo amene kale ankavala zokongolatsopano akugona pa phulusa.6Kuyipa kwa anthu anga kunali kwakukulukuposa anthu a ku Sodomu,amene anawonongedwa mʼkamphindi kochepapopanda owathandiza.7Akalonga ake anali owala koposa chisanu chowundanandi oyera kuposa mkaka.Matupi awo anali ofiira kuposa miyala ya rubi,maonekedwe awo ngati miyala ya safiro.8Koma tsopano maonekedwe awo ndi akuda kuposa mwaye;palibe angawazindikire mʼmisewu ya mu mzinda.Khungu lawo lachita makwinyamakwinya pa mafupa awo;lawuma gwaa ngati nkhuni.9Amene anaphedwa ndi lupanga aliko bwino kuposaamene anafa ndi njala;chifukwa chosowa chakudya cha mʼmundaiwowa ankafowoka ndi njala mpaka kufa.10Amayi achifundo afikapophika ana awo enieni,ndiwo anali chakudya chawo pamene anthuanga anali kuwonongeka.11Yehova wakwaniritsa ukali wake;wagwetsa pansi mkwiyo wake woopsa.Ndipo wayatsa moto mʼZiyonikuti uwononge maziko ake.12Mafumu a pa dziko lapansi sanakhulupirire,kapena wina aliyense wokhala pa dziko lonse,kuti adani kapena ankhondo akhoza kulowapa zipata za Yerusalemu.13Koma izi zinachitika chifukwa cha kuchimwa kwa aneneri akendi mphulupulu za ansembe ake,amene ankapha anthu osalakwa pakati pawo.14Tsopano akungoyendayenda mʼmisewu ya mu mzindangati anthu osaona.Iwo ndi odetsedwa kwambiri ndi magazipalibe yemwe angayerekeze nʼkukhudza komwe chovala chawo.15Anthu akuwafuwulira kuti, “Chokani! Inu anthu odetsedwa!”“Chokani! Chokani! Musatikhudze ife!”Akamathawa ndi kumangoyendayenda,pakati pa anthu a mitundu yonse amati,“Asakhalenso ndi ife.”16Yehova mwini wake wawabalalitsa;Iye sakuwalabadiranso.Ansembe sakulandira ulemu,akuluakulu sakuwachitira chifundo.17Ndiponso maso athu atopa nʼkuyangʼana,chithandizo chosabwera nʼkomwe,kuchokera pa nsanja zathu tinadikirira mtunduwa anthu umene sukanatipulumutsa.18Anthu ankalondola mapazi athu,choncho sitikanayenda mʼmisewu yathu mu mzinda.Chimaliziro chathu chinali pafupi, masiku athu anali owerengeka,chifukwa chimaliziro chathu chinali chitafika.19Otilondola akuthamanga kwambirikuposa ziwombankhanga mu mlengalenga;anatithamangitsa mpaka ku mapirindi kutibisalira mʼchipululu.20Wodzozedwa wa Yehova, mpweya wathu wotipatsa moyo,anakodwa mʼmisampha yawo.Tinaganiza kuti tidzakhala pansi pa mthunzi wakepakati pa mitundu ya anthu.21Kondwera ndi kusangalala, mwana wamkazi wa Edomu.Iwe amene umakhala mʼdziko la Uzi.Koma iwenso chikho chidzakupeza;udzaledzera mpaka kukhala maliseche.22Iwe mwana wamkazi wa Ziyoni, chilango chako chidzatha;Iye sadzatalikitsa nthawi yako ya ukapolo.Koma Yehova adzalanga machimo ako, iwe mwana wamkazi wa Edomu,ndi kuyika poyera mphulupulu zako.