MALIRO3nya_bib
1Ine ndine munthu amene ndaona masautsondi ndodo ya ukali wake.2Wandipititsa kutali ndipo wandiyendetsamu mdima osati mʼkuwala;3zoonadi anandikantha ndi dzanja lakemobwerezabwereza tsiku lonse.4Wakalambitsa khungu langa ndi mnofu wanga,ndipo waphwanya mafupa anga.5Wandizinga ndi kundizungulirandi zowawa ndi zolemetsa.6Wandikhazika mu mdimangati amene anafa kale.7Wandimangira khoma kotero kuti sindingathawe,wandimanga ndi maunyolo.8Ngakhale pamene ndifuwula kapena kupempha chithandizo,amakana pemphero langa.9Wanditsekera njira yanga ndi miyala yosema;ndipo wakhotetsa tinjira tanga.10Wandidikirira ngati chimbalangondo,wandibisalira ngati mkango.11Wandikokera pambali ndi kundingʼambangʼamba,ndipo wandisiya wopanda thandizo.12Wakoka uta wakendipo walunjikitsa mivi yake pa ine.13Walasa mtima wangandi mivi ya mʼphodo mwake.14Ndinakhala choseketsa cha anthu anga onse;amandinyodola mʼnyimbo zawo tsiku lonse.15Wandidyetsa zowawandipo wandimwetsa ndulu.16Wathyola mano anga ndi miyala;wandiviviniza mʼfumbi;17Wandichotsera mtendere;ndayiwala kuti kupeza bwino nʼchiyani.18Choncho ndikuti, “Ulemerero wanga wachokandi zonse zimene ndimayembekeza kwa Yehova.”19Kukumbukira masautso anga ndi kusowa pokhala,zili ngati zowawa ndi ndulu.20Ine ndikuzikumbukira bwino izi,ndipo moyo wanga wathedwa mʼkati mwanga.21Komabe ndimakumbukira zimenezi,nʼchifukwa chake ndili ndi chiyembekezo.22Ife sitinawonongekeretu chifukwa chikondi cha Yehova ndi chachikulu,ndi chifundo chake ndi chosatha.23Zimaoneka zatsopano mmawa uliwonse;kukhulupirika kwanu nʼkwakukulu.24Mu mtima mwanga ndimati, “Yehova ndiye zanga zonse;motero ndimamuyembekezera.”25Yehova ndi wabwino kwa amene amayembekezera Iye,kwa munthu amene amafunafuna Iyeyo;26nʼkwabwino kudikira chipulumutso chaYehova modekha.27Nʼkwabwino kuti munthu asenze golipamene ali wamngʼono.28Akhale chete pa yekha,chifukwa Yehova wamusenzetsa golilo.29Abise nkhope yake mʼfumbimwina chiyembekezo nʼkukhalapobe.30Apereke tsaya lake kwa iye amene angamumenye,ndipo amuchititse manyazi.31Chifukwa Ambuye satayiratuanthu nthawi zonse.32Ngakhale amabweretsa zowawa, Iye adzawachitira chifundo,chifukwa chikondi chake ndi chosatha.33Pakuti sabweretsa masautso mwadala,kapena zowawa kwa ana a anthu.34Kuphwanya ndi phazia mʼndende onse a mʼdziko,35kukaniza munthu ufulu wakepamaso pa Wammwambamwamba,36kumana munthu chiweruzo cholungama—kodi Ambuye saona zonsezi?37Kodi ndani angayankhule zinthu nʼkuchitikangati Ambuye sanavomereze?38Kodi zovuta ndi zabwino sizitulukamʼkamwa mwa Wammwambamwamba?39Kodi nʼchifukwa chiyani munthu aliyense wamoyo amadandaulaakalangidwa chifukwa cha machimo ake?40Tiyeni tisanthule ndi kuyesa njira zathu,ndipo tiyeni tibwerere kwa Yehova.41Tiyeni tikweze mitima yathu ndi manja athukwa Mulungu kumwamba ndipo tinene kuti:42“Ife tachimwa ndi kuwukirandipo inu simunakhululuke.43“Mwadzikuta ndi mkwiyo ndi kutilondola ndipomwatitha mopanda chifundo.44Mwadzikuta mu mtambokotero mapemphero athu sakukufikani.45Mwatisandutsa zinyatsi ndi zinyalalapakati pa mitundu ya anthu.46“Adani anthu atitsekulira pakamwa.47Ife tadzazidwa ndi mantha pakuti tagwa mʼdzenje,tapasuka ndi kuwonongedwa.”48Misozi mʼmaso mwanga ikungoti mbwembwembwechifukwa anthu anga akuwonongedwa.49Misozi idzatsika kosalekeza,ndipo sidzasiya,50mpaka Yehova ayangʼane pansikuchokera kumwamba ndi kuona.51Mtima wanga ukupweteka poona zimenezichifukwa cha akazi onse a mu mzinda.52Akundisaka ngati mbalame,amene anali adani anga, popanda chifukwa.53Ayesa kundipha pondiponya mʼdzenjendi kundiponya miyala;54madzi anamiza mutu wangandipo ndinkaganiza kuti imfa yayandikira.55Ndinayitana dzina lanu Inu Yehova,kuchokera mʼdzenje lozama.56Inu munamva kudandaula kwanga. “Mundimverekulira kwanga kopempha thandizo.”57Munafika pafupi pamene ndinakuyitanani,ndipo munati, “Usaope.”58Inu Ambuye munandiwombola ku mlandu wanga;munapulumutsa moyo wanga.59Yehova, mwaona zoyipa zimene andichitira.Mundiweruzire ndinu!60Mwaona kuzama kwa kubwezera kwawo,chiwembu chawo chonse pa ine.61Inu Yehova mwamva kunyoza kwawo,chiwembu chawo chonse pa ine,62manongʼonongʼo a adani angaondiwukira ine tsiku lonse.63Tawaonani! Kaya ali pansi kapena kuyimirira,akundinyoza mu nyimbo zawo.64Inu Yehova, muwabwezere chowayenera,chifukwa cha zimene manja awo achita.65Phimbani mitima yawo,ndipo matemberero anu akhale pa iwo!66Muwalondole mwaukali ndipomuwawonongeretu pa dziko lapansi.