YOSWA12nya_bib

Mayina a Mafumu Ogonjetsedwa

1Aisraeli anagonjetsa dziko lonse la kummawa kwa Yorodani, kuyambira ku chigwa cha Arinoni mpaka ku phiri la Herimoni pamodzi ndi dera lonse la kummawa kwa Araba. Iwo anatenga dzikoli kukhala lawo, ndipo mafumu a dzikoli anali awa:
2Sihoni mfumu ya Aamori, amene ankakhala mu Hesiboni. Iye analamulira kuyambira ku Aroeri mzinda umene uli mʼmphepete mwa mtsinje wa Arinoni, mpaka ku mtsinje wa Yaboki, umene uli mʼmalire mwa Aamori, kuphatikizanso theka la dziko la Giliyadi.3Iye ankalamuliranso dera la chigwa cha Yorodani kuyambira ku Nyanja ya Kinereti, kummawa ndi kumatsika mpaka ku Beti-Yesimoti, mzinda umene unali kummawa kwa Nyanja ya Mchere ndi kutsikabe kummwera mpaka pa tsinde pa phiri la Pisiga.
4Ogi mfumu ya mzinda wa Basani, amene anali mmodzi mwa otsala mwa Arefaimu. Iye ankakhala ku Asiteroti ndi Ederi.5Dera la ufumu wake linafika ku phiri la Herimoni, ku Saleka ndi dziko lonse la Basani mpaka ku malire ndi anthu a ku Gesuri Makati. Ufumu wake unaphatikizanso theka la Giliyadi mpaka ku malire a mfumu Sihoni ya ku Hesiboni.
6Mose mtumiki wa Yehova ndi Aisraeli anawagonjetsa ndipo anapereka dziko lawo kwa anthu a fuko la Rubeni, fuko la Gadi ndi theka la fuko la Manase kuti chikhale cholowa chawo.
7Yoswa ndi Aisraeli onse anagonjetsa mafumu onse okhala kumadzulo kwa mtsinje wa Yorodani kuyambira ku Baala-Gadi, ku chigwa cha Lebanoni mpaka ku phiri la Halaki, kumapita cha ku Seiri. Yoswa anagawira dzikolo mafuko a Israeli kuti likhale cholowa chawo.8Dziko limeneli linali dera la ku mapiri, chigwa cha kumadzulo, chigwa cha Yorodani, ku matsitso a kummawa, ndi dziko la chipululu la kummwera. Amene ankakhala mʼdzikoli anali Ahiti, Aamori, Akanaani, Aperezi, Ahivi ndi Ayebusi. Mafumu ake anali awa:
9mfumu ya Yerikoimodzimfumu ya Ai (kufupi ndi Beteliimodzi10mfumu ya Yerusalemuimodzimfumu ya Hebroniimodzi11mfumu ya Yarimutiimodzimfumu ya Lakisiimodzi12mfumu ya Egiloniimodzimfumu ya Gezeriimodzi13mfumu ya Debriimodzimfumu ya Gederiimodzi14mfumu ya Horimaimodzimfumu ya Aradiimodzi15mfumu ya Libinaimodzimfumu ya Adulamuimodzi16mfumu ya Makedaimodzimfumu ya Beteliimodzi17mfumu ya Tapuwaimodzimfumu ya Heferiimodzi18mfumu ya Afekiimodzimfumu ya Lasaroniimodzi19mfumu ya Madoniimodzimfumu ya Hazoriimodzi20mfumu ya Simuroni Meroniimodzimfumu ya Akisafuimodzi21mfumu ya Taanakiimodzimfumu ya Megidoimodzi22mfumu ya Kadesiimodzimfumu ya Yokineamu ku Karimeliimodzi23mfumu ya Dori ku Nafoti Doriimodzimfumu ya Goyini ku Giligalaimodzi24mfumu ya Tirizaimodzimafumu onse pamodzi analipo 31.