YONA
2
/
nya_bib
Pemphero la Yona
1
Yona ali mʼmimba mwa chinsomba chija anapemphera kwa Yehova Mulungu wake.
2
Iye anati:
“Pamene ndinali mʼmavuto anga ndinayitana Yehova,
ndipo Iye anandiyankha.
Ndili ku dziko la anthu akufa ndinapempha thandizo,
ndipo Inu munamva kulira kwanga.
3
Munandiponya mʼnyanja yozama,
mʼkati mwenimweni mwa nyanja,
ndipo madzi oyenda anandizungulira;
mafunde anu onse ndi mkokomo wake
zinandimiza.
4
Ndinati, ‘Ine ndachotsedwa
pamaso panu;
komabe ndidzayangʼananso
ku Nyumba yanu yopatulika.’
5
Madzi wondimiza anandichititsa mantha,
nyanja yozama inandizungulira;
udzu wa mʼmadzi zinakuta mutu wanga.
6
Ndinatsikira kunsi ndithu, mʼtsinde mwa mapiri;
mipiringidzo ya dziko inanditsekereza kosatha.
Koma Inu munatulutsa moyo wanga mʼmandamo,
Inu Yehova Mulungu wanga.
7
“Pamene moyo wanga umachoka mwa ine,
ine ndinakumbukira Inu Yehova,
ndipo pemphero langa linafika kwa inu,
ku Nyumba yanu yopatulika.
8
“Iwo amene amagwiritsitsa mafano achabechabe
amataya chisomo chawo.
9
Koma ine ndidzapereka kwa Inu nsembe
ndikuyimba nyimbo yamayamiko.
Chimene ndinalonjeza ndidzachikwaniritsa.
Chipulumutso chimachokera kwa Yehova.”
10
Ndipo Yehova analamula chinsomba chija, ndipo chinakamusanza Yonayo mʼmbali mwa nyanja.
Powered by Seed Bible API
expand_more
Search
All books
Old Testament
New Testament
chevron_left
Previous Chapter
Books
search
Search
explore
Discover
share
Share
chevron_right
Next Chapter