Yoweli1nya_bib

1Yehova anayankhula ndi Yoweli mwana wa Petueli.

Kubwera kwa Dzombe

2Inu akuluakulu, imvani izi;mvetserani, nonse amene mumakhala mʼdziko.Kodi zinthu zokhala ngati izi zinayamba zaonekapo mʼnthawi yanu,kapena mʼnthawi ya makolo anu?3Muwafotokozere ana anu,ndipo ana anuwo afotokozere ana awo,ndipo ana awo adzafotokozere mʼbado winawo.4Chimene dzombe losamera mapiko lasiyadzombe lowuluka ladya;chimene dzombe lowuluka lasiyadzombe lalingʼono ladya;chimene dzombe lalingʼono lasiyachilimamine wadya.
5Dzukani, inu zidakwa ndipo mulire!Lirani mofuwula, inu nonse amene mumamwa vinyo;lirani mofuwula chifukwa cha vinyo watsopano,pakuti wachotsedwa pakamwa panu.6Mtundu wa anthu wathira nkhondo dziko langa,wamphamvu ndi wosawerengeka;uli ndi mano a mkango,zibwano za mkango waukazi.7Wawononga mphesa zangandipo wathyola mitengo yanga ya mkuyu.Wakungunula makungwa akendi kuwataya,kusiya nthambi zake zili mbee.
8Lirani ngati namwali wovala chiguduli,chifukwa cha mwamuna wa utsikana wake.9Chopereka cha chakudya ndi cha chakumwasizikuperekedwa ku nyumba ya Yehova.Ansembe akulira,amene amatumikira pamaso pa Yehova.10Minda yaguga,nthaka yauma;tirigu wawonongeka,vinyo watsopano watha,mitengo ya mafuta yauma.11Khalani ndi nkhawa, inu alimi,lirani mofuwula inu alimi a mphesa;imvani chisoni chifukwa cha tirigu ndi barele,pakuti zokolola za mʼmunda zawonongeka.12Mpesa waumandipo mtengo wamkuyu wafota;makangadza, kanjedza ndi mitengo ya apulosi,mitengo yonse ya mʼmunda yauma.Ndithudi chimwemwe cha anthuchatheratu.

Mulungu Ayitana Anthu kuti Atembenuke

13Inu ansembe, valani ziguduli ndipo lirani;lirani mofuwula, inu amene mumatumikira pa guwa lansembe.Bwerani, fundani ziguduli usiku wonse,inu amene mumatumikira pamaso pa Mulungu wanga;pakuti chopereka cha chakudya ndi cha chakumwasizikupezekanso mʼnyumba ya Mulungu wanu.14Lengezani tsiku lopatulika losala zakudya,itanani msonkhano wopatulika.Sonkhanitsani akuluakulundi anthu onse okhala mʼdzikoku nyumba ya Yehova Mulungu wanundipo alirire Yehova.
15Kalanga ine tsikulo!Pakuti tsiku la Yehova layandikira;lidzabwera ngati chiwonongeko chochokera kwa Wamphamvuzonse.
16Kodi chakudya chathu sichachotsedwaife tikuona?Kodi mʼnyumba ya Mulungu wathusimulibe chimwemwe ndi chisangalalo?17Mbewu zikunyalapoti pansi ndi powuma.Nyumba zosungiramo zinthu zawonongeka;nkhokwe zapasukapopeza tirigu wauma.18Taonani mmene zikulirira ziweto;ngʼombe zikungoyenda uku ndi ukuchifukwa zilibe msipu;ngakhalenso nkhosa zikusauka.
19Kwa Inu Yehova ndilirira,pakuti moto wapsereza msipu wakuthengo,malawi amoto apsereza mitengo yonse ya mʼtchire.20Ngakhale nyama zakuthengo zikulirira Inu;timitsinje tonse taphwandipo moto wapsereza msipu wa kuthengo.