YOBU38nya_bib

Yehova Ayankhula

1Apo Yehova anamuyankha Yobu mʼkamvuluvulu. Ndipo anati:2“Kodi uyu ndani amene akusokoneza uphungu wangapoyankhula mawu opanda nzeru?3Onetsa chamuna;ndikufunsandipo undiyankhe.
4“Kodi unali kuti pamene ndinkayika maziko a dziko lapansi?Ndiwuze ngati ukudziwa.5Ndani amene analemba malire ake? Ndithudi iwe ukudziwa!Ndani amene anayeza ndi chingwe dzikoli?6Kodi maziko ake anawakumba potani,kapena ndani anayika mwala wake wapangodya,7pamene nyenyezi za kummawa zinkayimba pamodzindipo angelo onse a Mulungu ankafuwula mokondwa?
8“Kodi ndani amene anatsekera nyanja pamene inkalengedwa,pamene inkachita ngati kutumphuka pansi pa dziko,9pamene ndinasandutsa mitambo kukhala chovala chakendi kuyikulunga mu mdima wandiweyani,10pamene ndinayilembera malire akendikuyikira zitseko ndi mipiringidzo yake.11Pamene ndinati, ‘Ufike mpaka apa ndipo usapitirireapa ndiye pamene mafunde ako amphamvuwo azilekezera?’
12“Kodi chibadwire chako unalamulapo dzuwa kuti lituluke mmawa,kapena kuti mʼbandakucha ukhalepo pa nthawi yake,13kuti kuwalako kuwunikire dziko lonse lapansindi kuthamangitsa anthu oyipa?14Chifukwa cha kuwala kwa usana mapiri ndi zigwa zimaonekera bwino ngati zilembo za chidindo pa mtapo;zimaonekera bwino ngati makwinya a chovala.15Kuwala kwa dzuwako sikuwafikira anthu oyipa,ndipo dzanja lawo silingathe kuchita kanthu.
16“Kodi unayendapo pansi penipeni pa nyanjakapena pa magwero ake ozama?17Kodi anakuonetsapo zipata za imfa?Kodi unaonako ku dziko la anthu akufa kumene kuli mdima wandiweyani?18Kodi kukula kwa dziko lapansi umakudziwa?Undiwuze ngati ukuzidziwa zonsezi.
19“Kodi njira yopita kumene kumakhala kuwala ili kuti?Nanga mdima umakhala kuti?20Kodi iwe ungathe kuziperekeza kwawoko zimenezi?Kodi ukuyidziwa njira yopita kwawoko?21Ndithu, iwe ukuyidziwa, poti paja nthawi imeneyo nʼkuti utabadwa kale!Wakhala ndi moyo zaka zambiridi!
22“Kodi unalowamo mʼnyumba zosungira chisanu chowundanakapena unayionapo nyumba yosungira matalala,23zimene ndazisungira nthawi ya mavutondi nthawi yomenyana ndi ya nkhondo?24Kodi umadziwa njira ya kumene kumachokera chingʼaningʼanikapena njira ya kumene kumachokera mphepo ya kummawa imene ili pa dziko lonse lapansi?25Kodi ndani amene amakonza ngalande za mvula,nanga ndani anakonza njira yoyendamo mphenzi,26kuthirira madzi dziko limene sikukhala munthu,chipululu chopandamo munthu,27kukhutitsa nthaka yowuma yagwaandi kumeretsamo udzu?28Kodi mvula ili ndi abambo ake?Nanga madzi a mame anawabereka ndani?29Kodi madzi owundana anawabereka ndani?Ndani amene anabereka chisanu chochokera kumwamba30pamene madzi amawuma gwaa ngati mwala,pamene madzi a pa nyanja amazizira, nalimba kuti gwaa?
31“Kodi iwe ungayimitse kuyenda kwa nyenyezi?Kodi ungathe kuletsa kuyenda kwa nsangwe ndi akamwiniatsatana?32Kodi ungathe kuwongolera nyenyezi pa nyengo yakekapena kutsogolera nyenyezi yayikulu ya chimbalangondo pamodzi ndi ana ake?33Kodi malamulo a mlengalenga umawadziwa?Kodi ungathe kukhazikitsa ulamuliro wa Mulungu pa dziko lapansi?
34“Kodi iwe ungathe kulamula mitambokuti igwetse mvula ya chigumula?35Kodi ungathe kutumiza zingʼaningʼani kuti zingʼanime?Kodi zimabwera pamaso pako ndi kuti, ‘Tili pano?’36Kodi ndani anayika nzeru mu mtima,ndani analonga mʼmaganizo nzeru zomvetsa zinthu?37Wanzeru ndani amene angathe kuwerenga mitambo?Ndani angathe kupendeketsa mitsuko ya madzi akuthambo38pamene fumbi limasanduka matope,ndipo matopewo amawumbika?
39“Kodi ndani amawusakira chakudya mkango waukazindi kukhutitsa misona ya mikango40pamene ili khale mʼmapanga mwawokapena pamene ikubisala pa tchire?41Kodi amamupatsa khwangwala chakudya chake ndanipamene ana ake akulirira kwa Mulungundi kumayendayenda chifukwa chosowa zakudya?