YOBU14nya_bib
1“Munthu wobadwa mwa amayiamakhala masiku owerengeka ndipo ndi odzaza ndi mavuto okhaokha.2Amaphuka ngati duwa ndipo kenaka amafota;amathawa ngati mthunzi ndipo sakhalitsa.3Kodi munthu wotereyo nʼkumuyangʼanitsitsa?Kodi mungamubweretse pamaso panu kuti mumuzenge mlandu?4Ndani angatulutse chabwino mʼchoyipa?Palibe ndi mmodzi yemwe!5Masiku a munthu ndi odziwikiratu;munakhazikitsa chiwerengero cha miyezi yakendipo munamulembera malire amene sangathe kuwalumpha.6Choncho Inu mumufulatire ndipo mumuleke apumulekufikira atakondwera nawo moyo ngati munthu waganyu.7“Mtengo uli nacho chiyembekezo:ngati wadulidwa, udzaphukiransondipo nthambi zake sizidzaleka kuphukira.8Mizu yake ingathe kukalamba mʼnthakandipo chitsa chake nʼkuwola pa dothi,9koma pamene chinyontho chafika udzaphukirandipo udzaphuka nthambi ngati mtengo wanthete.10Koma munthu amafa nayikidwa mʼmanda,amapuma mpweya wotsiriza ndipo kutha kwake nʼkomweko.11Monga madzi amaphwera mʼnyanjakapena monga mtsinje umaphwera nuwuma,12momwemonso munthu amagona ndipo sadzukanso;mpaka zamlengalenga zidzathe, anthu sadzaukakapena kudzutsidwa ku tulo tawo.13“Aa, Inu mukanangondibisa mʼmandandi kundiphimba kuti ndisaoneke mpaka mkwiyo wanu utapita!Achikhala munandiyikira nthawi,kuti pambuyo pake mundikumbukirenso.14Munthu akafa, kodi adzakhalanso ndi moyo?Masiku anga onse a moyo wovutikawundidzadikira mpaka itafika nthawi yomasulidwa.15Inu mudzandiyitane ndipo ndidzakuyankhani;inu mudzafunitsitsa kuona cholengedwa chimene munachipanga ndi manja anu.16Ndithudi pamenepo mudzayangʼana mayendedwe angakoma simudzalondola tchimo langa.17Zolakwa zanga zidzakulungidwa mʼthumba;inu mudzaphimba tchimo langa.18“Koma monga phiri limakokolokera ndi kuswekaswekandipo monga thanthwe limasunthira kuchoka pa malo ake,19monganso madzi oyenda amaperesera miyalandipo madzi othamanga amakokololera nthaka,momwemonso Inu mumawononga chiyembekezo cha munthu.20Inu mumamugonjetsa kamodzinʼkamodzi ndipo munthuyo nʼkutheratu;Inu mumasintha maonekedwe a nkhope yake ndipo mumamutaya kutali.21Ana ake akamalemekezedwa, iyeyo sazidziwa zimenezo;akamachititsidwa manyazi iye saziona zimenezo.22Iye amangomva zowawa za mʼthupi lakendipo amangodzilirira yekha mwini wakeyo.”