YEREMIYA8nya_bib

1Yehova akuti, “ ‘Pa nthawi imeneyo, mafupa a mafumu ndi a akuluakulu a ku Yuda, mafupa a ansembe ndi a aneneri, ndiponso mafupa a anthu a ku Yerusalemu adzafukulidwa.2Adzawamwaza pa nthaka kuyangʼana dzuwa, mwezi ndi nyenyezi zonse zamlengalenga, zimene ankazikonda, kuzitumikira ndi kuzitsatira, kupemphako nzeru ndiponso kuzilambira. Mafupawo sadzawasonkhanitsa kapena kuwakwirira, koma adzakhala ngati ndowe pamwamba pa nthaka.3Otsala onse a mtundu woyipawu adzafuna imfa kopambana moyo kulikonse kumene ndidzawapirikitsirako, akutero Yehova Wamphamvuzonse.’ ”

Tchimo ndi Chilango Chake

4“Tsono awuze anthuwa, ‘Yehova akuti:“ ‘Kodi anthu akagwa sangadzukenso?Munthu akasochera kodi sangathe kubwereranso?5Chifukwa chiyani nanga anthu awa akupitirirabe kuchimwa, osabwerera?Chifukwa chiyani Yerusalemu akubwerera mʼmbuyo?Iwo akangamira chinyengo;akukana kubwerera.6Ine ndinatchera khutu kumvetserakoma iwo sanayankhulepo zoona.Palibe woyipa amene analapapo zoyipa zake,nʼkumati, ‘Ine ndachita chiyani?’Aliyense akutsatira njira yakengati kavalo wothamangira nkhondo.7Mbalame yotchedwa kakowa ija imadziwanthawi yake mlengalenga.Koma nkhunda, namzeze ndi chingaluzimadziwa nthawi yonyamukira ulendo,koma anthu anga sadziwamalamulo a Yehova.
8“ ‘Inu mukunena bwanji kuti,‘Ndife anzeru ndipo timasunga malamulo a Yehova?’Koma ndi alembi anuamene akulemba zabodza.9Anthu anzeru achita manyazi;athedwa nzeru ndipo agwidwa.Iwo anakana mawu a Yehova.Nanga tsono nzeru zawo ziwapinduliranji?10Nʼchifukwa chake akazi awo ndidzawapereka kwa amuna enandipo minda yawo ndidzayipereka kwa amene adzawagonjetse.Kuyambira wamngʼono mpaka wamkulu,onse ali ndi khalidwe lofuna kupeza chuma mwakuba.Aneneri pamodzi ndi ansembe omwe,onse amachita zachinyengo.11Iwo amapoletsa zilonda za anthu angapamwamba chabenʼkumati, ‘Mtendere, mtendere,’pamene palibe mtendere.12Kodi amachita manyazi akamachita zonyansazi?Ayi, alibe manyazi ndi pangʼono pomwe;iwo sadziwa nʼkugwetsa nkhope komwe.Choncho iwo adzagwera pakati pa anzawo amene agwa kale;adzagwa pansi tsiku limene ndidzawalanga,akutero Yehova.
13“ ‘Ndidzatenga zokolola zawo,Sipadzakhalanso mphesa pa mpesakapena nkhuyu pa mkuyu,ndipo masamba ake adzawuma.Zinthu zimene ndinawapatsandidzawachotsera.’ ”
14Koma amati, “Tikukhala pano chifukwa chiyani?Tiyeni tonse pamodzitithawire ku mizinda yotetezedwandi kukafera kumeneko.Pakuti Yehova Mulungu wathu watsimikiza kuti tiyenera kufa.Watipatsa madzi aululu kuti timwe,chifukwa tamuchimwira.15Tinkayembekezera mtenderekoma palibe chabwino chomwe chinachitika,tinkayembekezera kuchirakoma tinakumana ndi zoopsa zokhazokha.16Kulira kwa ngʼombe zazimuna za mdanikukumveka kuchokera ku Dani;dziko lonse likunjenjemerachifukwa cha kulira kwa akavalowo.Akubwera kudzawononga dzikondi zonse zimene zili mʼmenemo.Adzawononga mzinda ndi onse okhalamo.”
17Yehova akuti, “Onani, ndikukutumizirani njoka zaululu,mphiri zimene munthu sangathe kuzilodza,ndipo zidzakulumani,”
18Ndadzazidwa ndi chisoni kwambiri,mtima wanga walefukiratu.19Imvani kulira kwa anthu angakuchokera ku dziko lakutali:akuti, “Kodi Yehova sali ku Ziyoni?Kodi mfumu yake sili kumeneko?”“Chifukwa chiyani akundiputa ndi mafano awo osema,ndi milungu yawo yachilendo?”
20“Nthawi yokolola yapita,chilimwe chapita,koma sitinapulumuke.”
21Chifukwa cha mavuto a anthu anga, ine ndikumva kuwawa;ndikungolira ndipo mantha aakulu andigwira.22Kodi ku Giliyadi kulibe mankhwala ochiritsa?Kodi kumeneko kulibe singʼanga?Nanga chifukwa chiyani mabalaa anthu anga sanapole?