YEREMIYA48nya_bib
Uthenga Wonena za Mowabu
1Ponena za Mowabu:Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti,“Tsoka kwa mzinda wa Nebo, chifukwa wawonongedwa.Mzinda wa Kiriyataimu wachititsidwa manyazi ndipo wagonjetsedwa;linga lichititsidwa manyazi ndipo lagumulidwa.2Palibenso amene akutamanda Mowabu;ku Hesiboni anthu anamupanganira zoyipa:‘Bwerani, tiyeni timuwonongeretu kuti asakhalenso mtundu wa anthu.’Inunso anthu a ku Madimena, adzakukhalitsani chete;ankhondo adzakupirikitsani.3Tamvani mfuwu wa anthu a ku Horonaimu.Iwo akulira kuti, ‘Kusakazika ndi kuwonongeka kwakukulu.’4Mowabu wawonongeka;ana ake angʼonoangʼono akulira kwambiri.5Anthu akukwera chikweza cha ku Luhiti,akulira kwambiri pamene akupita.Kulira chifukwa cha chiwonongeko kukumvekapa njira yotsikira ku Horonaimu.6Thawani! Dzipulumutseni;khalani ngati mbidzi ya mʼchipululu.7Popeza inu munkadalira ntchito zanu ndi chuma chanu,nanunso mudzatengedwa ukapolo,ndipo Kemosi adzapita ku ukapolo,pamodzi ndi ansembe ake ndi akuluakulu ake.8Wowononga adzabwera ndi kusakaza mzinda uliwonse,ndipo palibe mzinda umene udzapulumuke.Chigwa chidzasanduka bwinjandipo malo athyathyathya a pamwamba pa phiri adzawonongedwamonga Yehova wayankhulira.9Mtsineni khutu Mowabuchifukwa adzasakazika;mizinda yake idzasanduka mabwinja,wopanda munthu wokhalamo.10“Wotembereredwa munthu amene amagwira ntchito ya Yehova monyinyirika!Wotembereredwa munthu amene amaletsa lupanga lake kupha anthu!11“Mowabu wakhala pa mtendere kuyambira ubwana wake,ngati vinyo wokhazikika pa masese ake,osapungulidwa kuchoka mu mtsuko wina kuthira mu mtsuko wina;iye sanatengedwepo ukapolo.Nʼchifukwa chake kukoma kwake nʼkomwe kujandipo fungo lake silinasinthe.12Nʼchifukwa chake masiku akubwera,”akutero Yehova,“pamene ndidzatuma anthu amene amakhuthula vinyo mʼmitsukondipo adzamukhutula;adzakhuthula vinyo yense mitsuko yakepambuyo pake nʼkuphwanya mitsukoyo.13Pamenepo Mowabu adzachita manyazi ndi Kemosi,monga momwe Aisraeli anachitira manyazindi Beteli amene ankamukhutulira.14“Kodi munganene bwanji kuti, ‘Ife ndife asilikali.Ife ndife ngwazi, anthu amphamvu pa nkhondo?’15Owononga Mowabu ndi mizinda yake abwera ndipo ankhondo adzalowa mʼmidzi yake;anyamata ake okongola apita kukaphedwa,”ikutero Mfumu, imene dzina lake ndi Yehova Wamphamvuzonse.16Kugwa kwa Mowabu kuli pafupi;masautso ake akubwera posachedwa.17Mulireni kwambiri, inu nonse amene mwamuzungulira,inu nonse amene mumadziwa za kutchuka kwake;nenani kuti, “Taonani momwe yathyokera ndodo yamphamvu yaufumu ija,taonani momwe ndodo yaulemu yathyokera!”18“Tsikani pa ulemerero wanundipo khalani pansi powuma,inu anthu okhala ku Diboni,pakuti wowononga Mowabuwabwera kudzamenyana nanu,wasakaza mizinda yanu yotetezedwa.19Inu amene mumakhala ku Aroeri,imani mʼmbali mwa msewu ndi kumaonerera.Funsani mwamuna amene akuthawa ndiponso mkazi amene wapulumuka,afunseni kuti, ‘Kodi chachitika nʼchiyani?’ ”20Iwo adzayankha kuti, “Mowabu wachititsidwa manyazi, pakuti wasakazika.Lirani mwachisoni ndipo fuwulani!Lengezani ku mtsinje wa Arinonikuti Mowabu wawonongedwa.21Chiweruzo chabwera ku mizinda ya ku mapiri,ndiyo Holoni, Yaza, Mefaati,22Diboni, Nebo, Beti-Dibilataimu,23Kiriyataimu, Beti-Gamuli, Beti-Meoni,24Keriyoti ndi Bozirandi mizinda yonse ya Mowabu, yakutali ndi yapafupi yomwe.25Mphamvu za Mowabu zawonongeka;mkono wake wathyoka,”akutero Yehova.26“Muledzeretseni Mowabu,chifukwa anadzikuza powukira Yehova.Mulekeni Mowabu avivinizike mʼmasanzi ake;mulekeni akhale chinthu chomachiseka.27Kodi suja Israeli anali kwa iwe ngati chinthu chomachiseka?Kodi Israeli anapezeka pakati pa akubakuti nthawi zonse poyankhula za iye,iwe uzimupukusira mutu momunyoza?28Inu amene mumakhala ku Mowabu,siyani mizinda yanu ndi kukakhala pakati pa matanthwe.Khalani ngati nkhunda imene imamanga chisa chakepa khomo la phanga.29“Tamva za kunyada kwa Mowabu,kunyada kwake nʼkwakukulu.Ndi wodzitama, wonyada ndi wodzitukumula.Ali ndi mtima wodzikweza.30Ine ndikuzidziwa ntchito zake,akutero Yehova.Ntchitozo ndi nʼzosapindulitsa kanthu.31Nʼchifukwa chake ndidzamulira Mowabu,ine ndikulira chifukwa cha anthu onse a ku Mowabu,ndikubuwula chifukwa cha anthu a ku Kiri Heresi.32Ndikukhetsa misozi chifukwa cha inu, kupambana momwe ndinalirira Yazeri.Inu anthu a ku Sibina muli ngati mipesaimene nthambi zake zatambalala mpaka ku Nyanja;zafika mpaka ku nyanja ya Yazeri.Wowononga wasakazazipatso zake zachilimwe ndi mpesa.33Chimwemwe ndi chisangalalo zathaku minda ya zipatso ya ku Mowabu.Ndaletsa kuchucha kwa vinyo mopsinyira mphesa;palibe amene akufuwula mokondwa akamapsinya mphesa.Ngakhale kufuwula kulipo,koma sikufuwula kwa chimwemwe.34“A ku Hesiboni ndi Eleali akulirandipo mfuwu wawo ukumveka mpaka ku Yahazi,kuchokera ku Zowari mpaka ku Horonaimu ndi ku Egilati Selisiya.Ngakhale madzi a ku Nimurimu aphwa.35Ndidzawaletsa anthu a ku Mowabukupereka nsembe mʼmalo awo opembedzerandi kufukiza lubani kwa milungu yawo,”akutero Yehova.36“Nʼchifukwa chake mtima wanga ukulirira Mowabu ngati chitoliro.Mtima wanga ukulirira anthu a ku Kiri Heresi ngati chitolirochifukwa chuma chimene anachipata chatha.37Aliyense wameta mutu wakendi ndevu zake;manja a munthu aliyense ndi ochekacheka,ndipo munthu aliyense wavala chiguduli mʼchiwuno mwake.38Pa madenga onse a ku Mowabundiponso mʼmisewu yakeanthu akungolira,pakuti ndaphwanya Mowabungati mtsuko wopanda ntchito,”akutero Yehova.39“Taonani mmene waphwanyikira! Tamvani momwe akulirira!Taonani momwe Mowabu wachititsidwira manyazi.Mowabu wasanduka chinthu chonyozeka,chinthu chochititsa mantha kwa onse amene amuzungulira.”40Yehova akuti,“Mtundu wina udzachita kuwuluka nʼkugwera pa Mowabu ngati chiwombankhangachimene chatambalitsa mapiko ake.41Mizinda idzagwidwandipo malinga adzalandidwa.Pa tsiku limenelo mitima ya ankhondo a ku Mowabuidzakhala ngati mtima wa mayi pa nthawi yake yochira.42Mowabu sudzakhala mtundu wa anthuchifukwa unadzikuza powukira Yehova.43Zoopsa, dzenje ndi msampha zikudikirainu anthu a ku Mowabu,”akutero Yehova.44“Aliyense wothawa zoopsaadzagwera mʼdzenje,aliyense wotuluka mʼdzenjeadzakodwa mu msampha.Ndigwetsa zimenezi pa Mowabupa nthawi ya chilango chake,”akutero Yehova.45“Anthu othawa nkhondo ayima pa mthunzi wa Hesibonichifukwa chotopa.Koma moto wayaka kuchokera ku Hesiboni,malawi a moto abuka kuchokera ku nyumba ya mfumu Sihoni.Motowo ukuwononga mapiri a ku Mowabu,dziko la anthu onyada.46Tsoka kwa iwe Mowabu!Anthu opembedza Kemosi awonongeka.Ana ako aamuna ndi aakaziatengedwa ukapolo.47“Komabe masiku akutsogolondidzabwezeranso Mowabu chuma chake,”akutero Yehova.Chiweruzo cha Mowabu chathera pamenepa.