1Uthenga umene Yehova anamupatsa mneneri Yeremiya wonena za Afilisti, Farao asanathire nkhondo Gaza ndi uwu:2Yehova akuti,“Taonani mmene madzi akubwerera kuchokera kumpoto;adzasanduka mtsinje wosefukira ndi a mkokomo.Adzasefukira mʼdziko monse ndi kumiza chilichonse mʼmenemo,mizinda ndi onse okhala mʼmenemo.Anthu adzafuwula;anthu onse okhala mʼdzikomo adzalira3akadzamva mgugu wa ngʼombe zazimuna zothamanga,phokoso la magaleta akendi kulira kwa mikombero yake.Makolo sadzatembenuka kuti athandize ana awo;manja awo adzangoti khoba.4Pakuti tsiku lafikalowononga Afilisti onsendi kupha onse otsala,onse amene akanatha kuthandiza Turo ndi Sidoni.Yehova ali pafupi kuwononga Afilisti,otsala ochokera ku zilumba za ku Kafitori.5Anthu a ku Gaza ameta mipala;anthu a ku Asikeloni akhala chete.Inu otsala a ku chigwa,mudzakhala mukudzichekacheka mpaka liti?6“Mukulira kuti, ‘Aa, lupanga la Yehova,kodi udzapumula liti?Bwerera mʼmalo ako;ukhale momwemo ndipo ukhale chete.’7Koma lupangalo lidzapumula bwanjipamene Yehova walilamulirakuti lithire nkhondoAsikeloni ndi anthu a mʼmbali mwa nyanja?”