YESAYA9nya_bib

Ufumu wa Mesiya

1Anthu amene anali ndi nkhawa, sadzakhalanso otaya mtima. Masiku amakedzana Mulungu ananyozetsa dziko la Zebuloni ndi dziko la Nafutali, koma kutsogolo kuno dera lonse la Galileya, limene lili dziko la anthu a mitundu ina, kuyambira ku nyanja yayikulu, mʼmbali mwa Yorodani, adzalisandutsa laulemu.2Anthu oyenda mu mdimaawona kuwala kwakukulu;kwa iwo okhala mʼdziko la mdima wandiweyanikuwunika kwawafikira.3Inu mwauchulukitsa mtundu wanundipo mwawonjezera chimwemwe chawo.Iwo akukondwa pamaso panu,ngati mmene anthu amakondwera nthawi yokolola,ngatinso mmene anthu amakondwerapamene akugawana zolanda ku nkhondo.4Monga munachitira pogonjetsa Amidiyani,inu mwathyola golilimene limawalemera,ndodo zimene amamenyera mapewa awo,ndiponso mikwapulo ya anthu owazunza.5Nsapato iliyonse ya munthu wankhondo,ndiponso chovala chilichonse chodonthekera magazizidzatenthedwa pa motongati nkhuni.6Chifukwa mwana watibadwira,mwana wamwamuna wapatsidwa kwa ife,ndipo ulamuliro udzakhala pa phewa lake.Ndipo adzamutcha dzina lake lakutiPhungu Wodabwitsa, Mulungu Wamphamvu,Atate Amuyaya, ndi Mfumu ya Mtendere.7Ulamuliro ndi mtendere wakezidzakhala zopanda malire.Iye adzalamulira ufumu wake ali pampando waufumu wa Davide,ndipo adzawukhazikitsa ndi kuwuchirikizamwa chiweruzo cholungama ndi pochita zachilungamokuyambira nthawi imeneyo mpaka muyaya.Ndi mtima wake wonse, Yehova Wamphamvuzonsewatsimikiza kuchita zimenezi.

Mkwiyo wa Yehova pa Israeli

8Ambuye atumiza mawu otsutsa Yakobo;ndipo mawuwo agwera pa Israeli.9Anthu onse okhala muEfereimu ndi okhala mu Samariya,adzadziwa zimenezi.Iwo amayankhula modzikuza kuti,10“Ngakhale njerwa zagumuka,koma ife tidzamanga ndi miyala yosema.Mitanda ya mkuyu yagwetsedwa,koma ife tidzayika mitanda ya mkungudza mʼmalo mwake.”11Koma Yehova wadzutsa adani kuti alimbane nawondipo wawafulumiza adani awo kuti amenyane nawo.12Asiriya ochokera kummawa ndi Afilisti ochokera kumadzulo ndipoayasama pakamwa kuti adye a Israeli.Komabe, mkwiyo wake sunawachokere,mkono wake uli chitambasulire.
13Koma anthu sanabwerere kwa amene anawakantha uja,ngakhale kufunafuna Yehova Wamphamvuzonse.14Choncho Yehova adzadula mutu wa Israeli pamodzi ndi mchira womwe,nthambi ya kanjedza ndi bango lomwe tsiku limodzi;15mutuwo ndiye akuluakulu ndi olemekezeka,mchira ndiye aneneri ophunzitsa zabodza.16Amene amatsogolera anthuwa ndiwo amawasocheretsa,ndipo otsogoleredwa amatayika.17Nʼchifukwa chake Ambuye adzakondwera nawo achinyamata,ngakhale kuwachitira chifundo ana amasiye ndi akazi amasiye,pakuti aliyense ndi wosapembedza Mulungu ndiponso ndi wochimwa ndipoaliyense amayankhula zopusa.Komabe, mkwiyo wake sunawachokere,mkono wake uli chitambasulire.
18Ndithu kuyipa kwa anthuwo kumayaka ngati moto;moto wake umanyeketsa mkandankhuku ndi minga,umayatsa nkhalango yowirira,ndipo utsi wake umachita kuti toloo ngati mtambo.19Dziko lidzatenthedwa ndi ukali wa Yehova Wamphamvuzonse,dziko lidzatenthedwandipo anthu adzakhala ngati nkhuni zosonkhera moto;palibe munthu amene adzachitire chifundo mʼbale wake.20Kudzanja lamanja adzapeza chakudya nʼkudya,koma adzakhalabe ndi njala;kudzanja lamanzere adzapeza chakudya nʼkudya,koma sadzakhuta.Aliyense azidzadya ana ake omwe.21Manase adzadya Efereimu ndipo Efereimu adzadya Manase;onsewa pamodzi adzadya Yuda.Komabe pa zonsezi, mkwiyo wake sunawachokere,mkono wake uli chitambasulire.