YESAYA65nya_bib

Chiweruzo ndi Chipulumutso

1“Ndinali wokonzeka kumva mapemphero a amene sankandipempha kanthu;ndipo ndinalola kuti anthu amene ankandifunafuna kuti andipeze.Kwa mtundu wa anthu umene sunkapempha chithandizo kwa Ine,ndinati, ‘Ine ndili pano, Ine ndili pano.’2Tsiku lonse ndatambasulira manja angaanthu owukira aja,amene amachita zoyipa,natsatira zokhumba zawo.3Ndatambasulira manja anga anthu aja amene nthawi zonse amandikwiyitsamopanda manyazi.Iwo amapereka nsembe mʼmindandi kufukiza lubani pa maguwa ansembe a njerwa.4Amakatandala ku mandandipo amakachezera usiku wonse kumalo obisika.Amadya nyama ya nkhumba,ndipo mʼmiphika mwawo muli msunzi wa nyama yodetsedwa.5Amawuza ena kuti, ‘Khala patali usandiyandikire,chifukwa ungatengere kupatulika kwanga!’Ukali wanga pa anthu otere uli ngati utsi mphuno zanga,ngati moto umene umayaka tsiku lonse.
6“Taonani, ndatsimikiza kale mlandu ndi chilango chawo;sindidzakhala chete koma ndidzawalanga kwathunthuchifukwa cha machimo awo7ndi a makolo awo,”akutero Yehova.“Chifukwa anapereka nsembe zopsereza pa mapirindi kundinyoza Ine pa zitunda zawo,Ine ndidzawalanga kwathunthu potsatazimene anachita kale.”8Yehova akuti,“Pamene madzi akanapezeka mu phava la mphesandipo anthu amati, ‘Musawononge phavalo,popeza madzi ena abwino akanalimobe mʼphavalo,’Inenso chifukwa cha mtumiki wanga;sindidzawononga onse.9Ndidzatulutsa zidzukulu mʼbanja la Yakobo,ndipo a banja la Yuda adzalandira mapiri anga ngati cholowa chawo.Anthu anga osankhidwa adzalandira zimenezi,ndipo atumiki anga adzakhala kumeneko.10Chigwa cha Saroni chidzakhala kodyetserako nkhosa,ndipo chigwa cha Akori chidzakhala malo opumirako ngʼombekwa anthu anga ondifunafuna Ine.
11“Koma inu amene mumasiya Yehovandi kuyiwala phiri langa lopatulika,amene munamukonzera Gadi chakudyandi kuthirira Meni chakumwa,12ndidzakuperekani ku lupanga ngati nsembe,ndipo nonse mudzaphedwa;chifukwa simunayankhe pamene ndinakuyitanani,ndinayankhula koma simunamvere.Munachita zoyipa pamaso pangandipo munasankha kuchita zoyipa zomwe sindikondwera nazo.”13Nʼchifukwa chake Ambuye Yehova akuti,“Atumiki anga adzadya,koma inu mudzakhala ndi njala;atumiki anga adzamwa,koma inu mudzakhala ndi ludzu;atumiki anga adzakondwa,koma inu mudzakhala ndi manyazi.14Atumiki anga adzayimbamosangalala,koma inu mudzalira kwambirichifukwa chovutika mu mtimandipo mudzalira mofuwula chifukwa mudzamva kuwawa mu mtima.15Anthu anga osankhidwaadzatchula dzina lanu potemberera.Ambuye Yehova adzakuphani,koma atumiki ake adzawapatsa dzina lina.16Aliyense wopempha dalitso mʼdzikomoadzachita zimenezo kwa Mulungu woona;ndipo aliyense wochita malumbiro mʼdzikomoadzalumbira mwa Mulungu woona.Pakuti mavuto akale adzayiwalikandipo adzachotsedwa pamaso panga.

Chilengedwe Chatsopano

17“Taonani, ndikulengamlengalenga mwatsopano ndi dziko lapansi latsopano.Zinthu zakale sizidzakumbukika,zidzayiwalika kotheratu.18Koma inu mukhale osangalala ndi okondwa mpaka muyayachifukwa cha zimene ndikulenga,pakuti ndikulenga Yerusalemu kukhala malo wosangalatsandipo anthu ake adzakhala achimwemwe.19Ine ndidzakondwa chifuwa cha Yerusalemundipo ndidzasangalala chifukwa cha anthu anga.Kumeneko sikudzamvekanso kulirandi mfuwu wodandaula.
20“Ana sadzafa ali akhandandipo nkhalamba zonse zidzakwaniritsa zaka zawo zonse.Wamngʼono mwa iwoadzafa ali ndi zaka 100.Amene adzalephere kufika zaka 100adzatengedwa kukhalawotembereredwa.21Anthu adzamanga nyumba ndi kukhalamo,adzadzala mpesa ndipo adzadya zipatso zake.22Sadzamanganso nyumba anthu ena nʼkukhalamo,kapena kudzala ndi ena nʼkudya.Pakuti anthu anga adzakhala ndi moyowautali ngati mitengo.Osankhidwa anga adzakondwera ndi ntchitoya manja awo nthawi yayitali.23Sadzagwira ntchito pachabekapena kubereka ana kuti aone tsoka;chifukwa adzakhala anthu odalitsidwa ndi Yehova,iwowo pamodzi ndi adzukulu awo omwe.24Ndidzawayankha ngakhale asanathe nʼkupempha komwe.Pamene akuyankhula kumene Ine ndidzakhala nditamva kale.25Mʼmbulu ndi mwana wankhosa wamkazi zidzadyera pamodzi.Mkango udzadya udzu monga ngʼombe,koma fumbi ndiye chidzakhale chakudya cha njoka.Pa phiri langa lopatulika sipadzakhalachinthu chopweteka kapena chowononga,”akutero Yehova.