YESAYA55nya_bib

Kuyitanidwa kwa Womva Ludzu

1“Bwerani, inu nonse amene muli ndi ludzu,bwerani madzi alipo;ndipo inu amene mulibe ndalamabwerani, mudzagule chakudya kuti mudye!Bwerani mudzagule vinyo ndi mkakaosalipira ndalama, osalipira chilichonse.2Chifukwa chiyani ndalama zanu mukuwonongera zinthu zimene samadya,ndipo mukuwononga malipiro anu pa zinthu zimene sizikhutitsa?Tamverani, mvetsetsani zimene ndikunena kuti mudye zimene zili zabwino;ndipo mudzisangalatse.3Tcherani makutu ndipo mubwere kwa Ine;mvereni Ine, kuti mukhale ndi moyo.Ndidzachita nanu pangano losatha,chikondi changa chija chosasinthika ndi chodalirika ndinalonjeza Davide.4Taonani, ine ndamusankha kuti akhale mboni yanga kwa mitundu ya anthu,kuti akhale mtsogoleri ndi wolamulira mitundu ya anthu.5Ndithu inu mudzayitanitsa mitundu ya anthu imene simuyidziwa,ndipo mitundu ya anthu imene sikudziwani idzabwera ndi liwiro kwa inu.Izi zidzatero chifukwa Yehova Mulungu wanu,Woyerayo wa Israeli,wakuvekani ulemerero.”
6Funafunani Yehova pamene Iye akupezeka.Mupemphere kwa Iye pamene ali pafupi.7Woyipa asiye makhalidwe ake oyipa,ndipo wosalungama asinthe maganizo ake oyipa.Abwerere kwa Yehova, ndipo adzamuchitira chifundo,ndi kwa Mulungu wathu, pakuti adzamukhululukira koposa.
8“Pakuti maganizo anga siwofanana ndi maganizo anu,ngakhale njira zanu si njira zanga,”akutero Yehova.9“Monga momwe mlengalenga muli kutali ndi dziko lapansi,momwemonso zochita zanga nʼzolekana kutali ndi zochita zanu,ndipo maganizo anga ndi osiyana kutali ndi maganizo anu.10Monga mvula ndi chisanu chowundanazimatsika kuchokera kumwamba,ndipo sizibwerera komwekokoma zimathirira dziko lapansi.Ndipo zimameretsa ndi kukulitsa zomerakenaka nʼkupatsa mlimi mbewu ndi chakudya.11Ndi mmenenso amachitira mawu ochokera mʼkamwa mwanga.Sadzabwerera kwa Ine kopanda phindu lake,koma adzachita zonse zimene ndifuna,ndipo adzakwaniritsa cholinga chimene ndinawatumira.12Inu mudzatuluka mu mzindawo mwachimwemwendipo adzakutsogolerani mwamtendere;mapiri ndi zitundazidzakuyimbirani nyimbo,ndipo mitengo yonse yamʼthengoidzakuwombereni mʼmanja.13Mʼmalo mʼmene tsopano muli mitengo ya minga mudzamera mitengo ya payini,ndipo kumene kuli mkandankhuku kudzamera mchisu.Zimenezi zidzakhala chikumbutso cha Yehova,ngati chizindikiro chamuyaya,chimene sichidzafafanizika konse.”