YESAYA52nya_bib
1Dzambatuka, dzambatuka iwe Ziyoni,vala zilimbe.Vala zovala zako zokongola,iwe Yerusalemu, mzinda wopatulika.Pakuti kuyambira tsopano anthu osachita mdulidwe ndi odetsedwasadzalowanso pa zipata zako.2Sasa fumbi lako;imirira nukhale pa mpando waufumu, iwe Yerusalemu.Inu omangidwa a ku Ziyoni,masulani maunyolo amene ali mʼkhosi mwanumo.3Pakuti Yehova akuti,“Sindinalandirepo kanthu pamene ndinakugulitsani,choncho mudzawomboledwa wopanda ndalama.”4Pakuti Ambuye Yehova akuti,“Poyamba paja anthu anga anapita kukakhala ku Igupto;nawonso Asiriya awapondereza popanda chifukwa.”5Tsopano Ine Yehova ndikuti,“Kodi nditani pakuti anthu anga atengedwa ukapolo osaperekapo kanthu,amene amawalamulira amawanyoza,”akutero Yehova.“Ndipo tsiku lonse, akungokhalirakuchita chipongwe dzina langa.6Tsono tsiku limenelo anthu anga adzadziwa dzina langa;kotero adzadziwakuti ndi Ine amene ndikuyankhula,Indedi, ndine.”7Ngokongoladi mapazi aamithenga obweretsa nkhani yabwino amene akuyenda pa mapiri.Iwo akukubweretserani nkhani zabwino za mtendere,chisangalalo ndi chipulumutso.Iwo akubwera kudzawuza anthua ku Ziyoni kuti,“Mulungu wako ndi mfumu!”8Mverani! Alonda anu akukweza mawu awo;akuyimba pamodzi mwachimwemwe.Popeza akuona chamasokubwera kwa Yehova ku Yerusalemu.9Imbani pamodzi mofuwula nyimbo zachimwemwe,inu mabwinja a Yerusalemu,pakuti Yehova watonthoza mtima anthu ake,wapulumutsa Yerusalemu.10Yehova wagwiritsa ntchito mphamvu zake zopatulikapamaso pa anthu a mitundu yonse,ndipo anthu onse a dziko lapansiadzaona chipulumutso cha Mulungu wathu.11Nyamukani, nyamukani, chokaniko ku Babuloniko!Musakhudze kanthu kodetsedwa!Inu amene mumanyamula ziwiya za Yehovatulukanimo ndipo mudziyeretse.12Koma simudzachoka mofulumirakapena kuchita chothawa;pakuti Yehova adzayenda patsogolo panu,Mulungu wa Israeli adzakutetezani kumbuyo kwanu.