YESAYA47nya_bib

Kugwa kwa Babuloni

1“Tsika, ndi kukhala pa fumbi,iwe namwali, Babuloni;khala pansi wopanda mpando waufumu,iwe namwali, Kaldeyapakuti sadzakutchulanso wanthete kapena woyenerakumugwira mosamala.2Tenga mphero ndipo upere ufa;chotsa nsalu yako yophimba nkhopekwinya chovala chako mpaka ntchafundipo woloka mitsinje.3Maliseche ako adzakhala poyerandipo udzachita manyazi.Ndidzabwezera chilangondipo palibe amene adzandiletse.”
4Woyerayo wa Israeli ndiye Mpulumutsi wathu,dzina lake ndi Yehova Wamphamvuzonse.
5“Khala chete, ndipo lowa mu mdima,iwe namwali, Kaldeya;chifukwa sadzakutchulansomfumukazi ya maufumu.6Ndinawakwiyira anthu anga,osawasamalanso.Ndinawapereka manja mwako,ndipo iwe sunawachitire chifundo.Iwe unachitira nkhanzangakhale nkhalamba.7Iwe unati, ‘Ine ndidzakhalapo nthawi zonsengati mfumukazi.’Koma sunaganizire zinthu izikapena kusinkhasinkha za mmene ziti zidzathere.
8“Ndipo tsopano, tamvera, iwe wongokonda zokondweretsawe,amene ukukhala mosatekesekawe,umaganiza mu mtima mwako kuti,‘Ine ndi Ine, ndipo kupatula ine palibenso wina.Sindidzakhala konse mkazi wamasiye,ndipo ana anga sadzamwalira.’9Koma mʼkamphindi, ndiponso tsiku limodzi,zinthu ziwiri izi zidzakuchitikira:ana ako kukufera komanso kukhala mkazi wamasiye.Zimenezi zidzakuchitikira kwathunthungakhale ali ndi amatsenga ambirindi mawula amphamvu.10Iwe unkadalira kuyipa kwakondipo unati, ‘Palibe amene akundiona.’Kuchenjera ndi nzeru zako zidzakusokoneza,choncho ukuganiza mu mtima mwako kuti,‘Ine ndine basi, ndipo kupatula ine palibenso wina.’11Ngozi yayikulu idzakugwerandipo sudzadziwa momwe ungayipewere ndi matsenga ako.Mavuto adzakugwerandipo sudzatha kuwachotsa;chipasupasu chimene iwe sukuchidziwachidzakugwera mwadzidzidzi.
12“Pitiriza tsono kukhala ndi matsenga ako,pamodzi ndi nyanga zako zochulukazo,wakhala ukuzigwiritsa ntchito kuyambira ubwana wako.Mwina udzatha kupambanakapena kuopsezera nazo adani ako.13Malangizo onse amene unalandira angokutopetsa basi!Abwere patsogolopa anthu amene amatanthauzira za kumwamba kuti adzakupulumutseni.Abwere amene amayangʼana nyenyezi, ndi kumalosera mwezi ndi mwezizimene ziti zidzakuchitikire.14Ndithudi, anthuwo ali ngati phesi;adzapsa ndi moto.Sangathe kudzipulumutsa okhaku mphamvu ya malawi a moto.Awa si makala a moto woti wina nʼkuwotha;kapena moto woti wina nʼkuwukhalira pafupi.15Umu ndi mmene adzachitire amatsenga,anthu amene wakhala ukugwira nawo ntchitondi kuchita nawo malonda chiyambire cha ubwana wako.Onse adzamwazika ndi mantha,sipadzakhala ndi mmodzi yemwe wokupulumutsa.”