YESAYA40nya_bib

Mawu a Chitonthozo kwa Anthu a Mulungu

1Atonthozeni, atonthozeni anthu anga,akutero Mulungu wanu.2Ayankhuleni moleza mtima anthu a ku Yerusalemundipo muwawuzitsekuti nthawi ya ukapolo wawo yatha,tchimo lawo lakhululukidwa.Ndawalanga mokwanirachifukwa cha machimo awo onse.
3Mawu a wofuwula mʼchipululu akuti,“Konzani njira ya Yehovamʼchipululu;wongolani njira zake;msewu owongoka wa Mulungu wathu mʼdziko lopanda kanthu.4Chigwa chilichonse achidzaze.Phiri lililonse ndi chitunda chilichonse azitsitse;Dziko lokumbikakumbika alisalaze,malo azitundazitunda awasandutse zidikha.5Ndipo ulemerero wa Yehova udzaonekera,ndipo mitundu yonse ya anthu idzawuona,pakuti wanena zimenezi ndi Yehova.”
6Wina ananena kuti, “Lengeza.”Ndipo ine ndinati, “Kodi ndifuwule chiyani?“Pakuti anthu onse ali ngati udzundipo kukongola kwawo kuli ngati maluwa akuthengo.7Udzu umanyala ndipo maluwa amafotachifukwa cha kuwomba kwa mpweya wa Yehova.”Mawu aja anatinso, “Ndithudi anthu sasiyana ndi udzu.8Udzu umanyala ndipo maluwa amafota,koma mawu a Mulungu wathu adzakhalapo mpaka muyaya.”
9Iwe amene ukulengeza nkhani yabwino ku Ziyoni,kwera pa phiri lalitali.Iwe amene ukulengeza nkhani yabwino ku Yerusalemu,fuwula kwambiri,kweza mawu, usachite mantha;uza mizinda ya ku Yuda kuti,“Mulungu wanu akubwera!”10Taonani, Ambuye Yehova akubwera mwamphamvu,ndipo dzanja lake likulamulira,taonani akubwera ndi mphotho yakewatsogoza zofunkha zako za ku nkhondo.11Iye adzasamalira nkhosa zake ngati mʼbusa:Iye adzasonkhanitsa ana ankhosa aakazi mʼmanja mwakendipo Iye akuwanyamula pachifuwa chakendi kutsogolera bwinobwino nkhosa zoyamwitsa.
12Kodi ndani akhoza kuyeza kuchuluka kwa madzi a mʼnyanja ndi chikhatho chake,kapena kuyeza kutalika kwa mlengalenga ndi dzanja lake?Ndani akhoza kuyeza dothi lonse la dziko lapansi mʼdengu,kapena kuyeza kulemera kwamapiri ndi zitunda ndi pasikelo?13Ndani anapereka malangizo kwa Mzimu wa Yehovakapena kumuphunzitsa Iye monga phungu wake?14Kodi Yehova anapemphapo nzeru kwa yani kuti akhale wopenya,kapena kuti aphunzire njira yoyenera ndi nzeru?Iye anapempha nzeru kwa yanindi njira ya kumvetsa zinthu?
15Ndithudi mitundu ya anthu ili ngati dontho la madzi ochoka mu mtsuko.Iwo akungoyesedwa ngati fumbi chabe pa sikelo;mʼmanja mwa Yehova zilumba nʼzopepuka ngati fumbi.16Nkhalango ya ku Lebanoni singakwanire nkhuni zosonkhera moto pa guwa lansembe,ngakhale nyama zake sizingakwanire kupereka nsembe zopsereza.17Pamaso pa Yehova mitundu yonse ya anthu ili ngati chinthu chopandapake;Iye amayiwerengera ngati chinthu chopanda phindundi cha chabechabe.
18Kodi tsono Mulungu mungamuyerekeze ndi yani?Kodi mungamufanizire ndi chiyani?19Likakhala fano, mʼmisiri ndiye analipangandipo mʼmisiri wa golide amalikuta ndi golidenaliveka mkanda wasiliva.20Mʼmphawi amene sangathe kupeza ngakhale chopereka nsembe chotereamasankha mtengo umene sudzawola,nafunafuna mʼmisiri waluso wotiamupangire fano limene silingasunthike.
21Kodi simukudziwa?Kodi simunamve?Kodi sanakuwuzeni kuyambira pachiyambi pomwe?Kodi simunamvetsetse chiyambire cha dziko lapansi?22Yehova amene amakhala pa mpando wake waufumu kumwamba ndiye analenga dziko lapansi,Iye amaona anthu a dziko lapansi ngati ziwala.Ndipo anafunyulula mlengalenga ngati nsalu yotchinga,nayikunga ngati tenti yokhalamo.23Amatsitsa pansi mafumu amphamvunasandutsa olamula a dziko kukhala achabechabe.24Inde, iwo ali ngati mbewu zimene zangodzalidwa kumenekapena kufesedwa chapompano,ndi kungoyamba kuzika mizu kumenendi pamene mphepo imawombapo nʼkuziwumitsandipo kamvuluvulu amaziwulutsa ngati mankhusu.
25Woyera uja akuti, “Kodi mudzandiyerekeza Ine ndi yani?Kapena kodi alipo wofanana nane?”26Tayangʼanani mlengalenga ndipo onani.Kodi ndani analenga zonsezi mukuzionazi?Yehova ndiye amene amazitsogolera ngati gulu la ankhondo,nayitana iliyonse ndi dzina lake.Ndipo popeza Iye ali ndi nyonga zambiri,palibe ndi imodzi yomwe imene inasowapo.
27Iwe Yakobo, chifukwa chiyani umanenandi kumadandaula iwe Israeli, kuti,“Yehova sakudziwa mavuto anga,Mulungu wanga sakusamala zomwe zikundichitikira ine?”28Kodi simukudziwa?Kodi simunamve?Yehova ndiye Mulungu wamuyaya,ndiyenso Mlengi wa dziko lonse lapansi.Iye sadzatopa kapena kufowokandipo palibe amene angadziwe maganizo ake.29Iye amalimbitsa ofowokandipo otopa amawawonjezera mphamvu.30Ngakhale achinyamata amalefuka ndi kufowoka,ndipo achinyamata amapunthwa ndi kugwa;31koma iwo amene amakhulupirira Yehovaadzalandira mphamvu zatsopano.Adzawuluka ngati chiwombankhanga;adzathamanga koma sadzalefuka,adzayenda koma sadzatopa konse.