YESAYA3nya_bib

Chiweruzo pa Yerusalemu ndi Yuda

1Taonani tsopano, AmbuyeYehova Wamphamvuzonse,ali pafupi kuchotsa mu Yerusalemu ndi mu Yudazinthu pamodzi ndi thandizo;adzachotsa chakudya chonse ndi madzi onse,2anthu amphamvu ndi asilikali ankhondo,oweruza ndi aneneri,anthu olosera ndi akuluakulu,3atsogoleri a ankhondo makumi asanu ndi anthu olemekezeka,aphungu ndi anthu amatsenga ndi akatswiri pa za kulosera.
4Ndidzawayikira anyamata kuti akhale mafumu awo;ana akhanda ndiwo adzawalamulire.5Anthu adzazunzana,munthu ndi munthu mnzake, mnansi ndi mnansi wake.Anthu wamba adzanyozaakuluakulu.
6Munthu adzagwira mʼbale wakemʼnyumba ya abambo awo, ndipo adzati,“Iwe uli nawo mwinjiro, ndiye ukhale mtsogoleri wathu;lamulira malo opasuka ano!”7Koma tsiku limenelo mʼbale wakeyo adzafuwula kuti,“Ayi, mavuto oterewa ndilibe mankhwala ake.Ndilibe chakudya kapena chovala mʼnyumba mwanga;musasankhe ine kukhala mtsogoleri wa anthu.”
8Yerusalemu akudzandira,Yuda akugwa;zokamba zawo ndi ntchito zawo nʼzotsutsana ndi Yehova,sakulabadira ulemerero wa Mulungu.9Maonekedwe a nkhope zawo amawatsutsa;amaonetsera poyera tchimo lawo ngati Sodomu;salibisa tchimo lawolo.Tsoka kwa iwoodziputira okha mavuto.
10Nena kwa olungama kuti zonse zidzawayendera bwino,pakuti adzakondwera ndi phindu la ntchito zawo.11Tsoka kwa anthu oyipa! Mavuto ali pa iwo!Adzalandira malipiro a zimene manja awo anachita.
12Achinyamata akupondereza anthu anga,ndipo amene akuwalamulira ndi akazi.Aa, anthu anga, atsogoleri anu akukusocheretsani;akukuchotsani pa njira yanu.
13Yehova wakhala pamalo pake mʼbwalo la milandu;wakonzeka kuti aweruze anthu ake.14Yehova akuwazenga milanduakuluakulu ndi atsogoleri a anthu ake:“Ndinu amene mwawononga munda wanga wa mpesa;nyumba zanu zadzaza ndi zolanda kwa amphawi.15Nʼchifukwa chiyani inu mukupsinja anthu anga,nʼkudyera masuku pamutu amphawi?”Akutero Ambuye Yehova Wamphamvuzonse.
16Yehova akunena kuti,“Akazi a ku Ziyoni ngodzikuza kwambiri,akuyenda atakweza makosi awo,akukopa amuna ndi maso awoakuyenda monyangʼamaakuliza zigwinjiri za mʼmiyendo yawo17Nʼchifukwa chake Ambuye, adzatulutsa zipere pa mitu ya akazi a ku Ziyoniwo;Yehova adzachititsa dazi mitu yawo.”18Tsiku limenelo Ambuye adzawachotsera zodzikongoletsera zawo: za mʼmiyendo, za ku mutu za mʼkhosi,19ndolo ndi zibangiri, nsalu zophimba pa nkhope,20maduku, zigwinjiri za mʼmiyendo ndi malamba, mabotolo a zonunkhira ndi zithumwa,21mphete ndi zipini,22zovala za pa mphwando, zipewa ndi mwinjiro, zikwama,23magalasi oyangʼanira, zovala zosalala, nduwira ndiponso nsalu za mʼmapewa.24Mʼmalo mwa kununkhira azidzanunkha,mʼmalo mwa lamba, adzavala chingwe;mʼmalo mwa tsitsi lopesa bwino, adzakhala ndi dazi;mʼmalo mwa zovala zabwino, adzavala chiguduli;mʼmalo mwa kunyadira kukongola adzachita manyazi.25Iwe Yerusalemu anthu ako aamuna adzaphedwa ndi lupanga,asilikali ako adzafera ku nkhondo.26Pa zipata za Ziyoni padzakhala kubuma ndi kulira;Iweyo udzasakazidwa nʼkukhala pansi, ukugubuduzika pa fumbi.