YESAYA26nya_bib

Nyimbo ya Matamando

1Tsiku limenelo anthu a mʼdziko la Yuda adzayimba nyimbo iyi.Tili ndi mzinda wolimba.Mulungu amawuteteza ndi zipupandi malinga.2Tsekulani zipata za mzindakuti mtundu wolungamandi wokhulupirika ulowemo.3Inu mudzamupatsa munthuwa mtima wokhazikikamtendere weniweni.4Mudalireni Yehova mpaka muyaya,chifukwa Yehova Mulungu ndiye Thanthwe losatha.5Iye amatsitsa anthu amene amadziyika pamwamba,iye amagwetsa pansi mzinda wodzitukumula,amagumula makoma akendi kuwagwetsa pansi pa fumbi penipeni.6Mapazi a anthu akuwupondereza,mapazi a anthu oponderezedwa,mapazi anthu osauka.
7Njira ya munthu wolungama ndi yosalaza,Inu Wolungamayo, mumasalaza njira ya wolungama.8Inde Yehova, timayenda mʼnjira zanu zolungama,ife timayembekezera Inu;mitima yathu imakhumba kukumbukirandi kulemekeza dzina lanu.9Moyo wanga umalakalaka Inu usiku wonse;nthawi yammawa ndimafunafuna Inu.Pamene muweruza dziko lapansianthu amaphunzira kuchita chilungamo.10Ngakhale mukomere mtima anthu oyipa,saphunzira chilungamo.Amachita zoyipa mʼdziko la chilungamo,ndipo sazindikira ululu wa Yehova.11Inu Yehova, mwatukula dzanja lanu kuti muwalange,koma iwo sakuliona dzanjalo.Aloleni anthu aone ndi kuchita manyazi poona mmene mukondera anthu anu;ndipo moto umene mwasonkhera adani anu uwapsereze.
12Yehova, mumatipatsa mtendere;ndipo zonse zimene ife tinazichita munatichitira ndinu.13Inu Yehova Mulungu wathu, ngakhale takhala tikulamulidwa ndi ena mʼmalo mwanu,koma ife timalemekeza dzina lanu lokha.14Iwo tsopano sadzadzukanso;mizimu yawo sidzabwera kudzativutitsapakuti mwawalanga ndipo mwawawononga;palibenso amene amawakumbukira.15Inu Yehova, mwaukulitsa mtundu wathu;mwauchulukitsa ndithundipo mwalandirapo ulemu;mwaukuza mbali zonse za dziko.
16Yehova, anthu anu anabwera kwa Inu pamene anali mʼmasautso;pamene munawalanga,iwo anapemphera kwa Inu.17Monga mayi woyembekezera pamene nthawi yake yobereka yayandikiraamamva kupweteka ndipo amalira ndi ululu,ifenso tinali chimodzimodzi pamaso panu, Inu Yehova.18Ife chimodzimodzi tinamva ululu, ngati mayi pa nthawi yobala mwana,koma sitinapindulepo kanthu,kapena kupulumutsa dziko lapansi;sitinabadwitse anthu atsopano pa dziko pano.
19Koma anthu anu amene anafa adzakhalanso ndi moyo;matupi awo adzadzuka.Iwo amene ali ku fumbi tsopanoadzadzuka ndi kuyimba mosangalala.Monga mame amafewetsa pansi kutsitsimutsa zomera,momwenso Yehova adzaukitsa anthu amene anafa kale.
20Abale anga, pitani mukalowe mʼnyumba zanundipo mukadzitsekere;mukabisale kwa kanthawi kochepampaka ukali wake utatha.21Taonani, Yehova akubwera kuchokera kumene amakhala;akubwera kudzalanga anthu a dziko lapansi chifukwa cha machimo awo.Dziko lapansi lidzawulula magazi amene anakhetsedwa pa dzikolo;dziko lapansi silidzabisanso mitembo ya anthu ophedwa.