YESAYA25nya_bib

Nyimbo Yotamanda Yehova

1Yehova ndinu Mulungu wanga;ine ndidzakukwezani ndi kutamanda dzina lanu,pakuti mwachita zodabwitsazimene munakonzekeratu kalekalemokhulupirika kwambiri.2Inu mwasandutsa mzinda uja kukhala mulu wamiyala.Ndipo mzinda wamalinga wasanduka bwinja,linga la anthu achilendo lero si mzindansondipo sidzamangidwanso.3Nʼchifukwa chake anthu amphamvu adzakulemekezani;mizinda ya mitundu ya anthu ankhanza idzakuopani.4Inu mwakhala ngati populumukira pa anthu osauka,mwakhala ngati kobisalirako munthu wovutika pa nthawi ya masautso ake.Mwakhala ngati pobisalirapopa nthawi ya mphepo yamkuntho ndi mthunzi pa nthawi ya dzuwa.Pakuti anthu ankhanzaali ngati mphepo yamkuntho yowomba pa khoma,5ndiponso ngati kutentha mʼdziko lowuma.Inu mumaletsa phokoso la anthu achilendo.Monga momwe mthunzi wa mtambo umachepetsa kutentha,inu munaletsa nyimbo za anthu ankhanza.
6Pa phiri ili Yehova Wamphamvuzonse adzakonzeraanthu a mitundu yonse madyerero a zakudya zokoma ndi vinyo wabwino.Phwando la nyama yononandi vinyo wabwino kwambiri.7Iye adzachotsa kulirakumene kwaphimba anthu ngati nsalu.Adzachotsa chinsalu chimene chakuta mitundu yonse ya anthu.8Yehova adzathetsa imfa mpaka muyaya,Ambuye Yehova adzapukuta misozi mʼmasomwa munthu aliyense;adzachotsa manyazi a anthu akepa dziko lonse lapansi,Yehova wayankhula.9Tsiku limenelo iwo adzati,“Ndithudi, uyu ndiye Mulungu wathu;ife tinamudalira ndipo anatipulumutsa.Uyu ndiye Yehova, ife tinamudalira;tiyeni tikondwe ndi kusangalala chifukwa watipulumutsa.”
10Yehova adzateteza phiri limeneli ndi dzanja lake;ndipo Amowabu adzawapondereza pomwe alilipo,ngati mmene amapondera manyowa mʼdzenje.11Amowabuwo adzatambasula manja awo mʼmenemo,ngati mmene amachitira munthu wosambira.Koma Mulungu adzathetsa kunyada kwawongakhale luso la manja awo.12Iye adzagumula malinga awo ataliatalindipo adzawagwetsandi kuwaponya pansi,pa fumbi penipeni.