YESAYA16nya_bib

1Anthu a ku Mowabuatumiza mphatso za ana ankhosa onenepa,kuchokera ku Sela kudutsa chipululumpaka kukafika ku phiri la Ziyoni.2Monga momwe mbalame zimawulukira uku ndi ukuakazimwaza mʼchisa,momwemonso akazi a ku Mowabuakuyendayenda ku madooko a Arinoni.
3Amowabu aja anawuza a ku Yuda kuti,“Tiwuzeni chochita, gamulani zoti tichite.Inu mutiteteze kwa adani anthu.Mukhale ngati mthunzi wathu dzuwa lili pa liwombo.Mutibise,musatipereke ife othawa nkhondo kwa adani athu.4Lolani kuti anthu othawa nkhondo a ku Mowabu azikhala pakati panu;mukhale populumukira pawo kwa wowonongayo.”Nthawi idzafika ndipo wozunzayo sadzakhalaponso,kuwononga kudzaleka;waukaliyo adzachoka mʼdzikomo.5Mpando waufumu udzakhazikitsidwa mwachikondi;mmodzi mwa zidzukulu za Davide adzakhalapo mokhulupirika.Iyeyo poweruza adzatsata chilungamondipo adzalimbikitsa kuchita zachilungamo.
6Tinamva kuti Mowabu anadzikuza kwambiri.Kunyada kwawondi kunyogodola kwawo ndi kudzitama kwawo,zonse ndi zopanda phindu.7Nʼchifukwa chake Amowabu akulira kwambiri;iwo akulirira dziko lawo.Akubuma momvetsa chisonichifukwa cha makeke a mphesa a ku Kiri Hareseti.8Minda ya ku Hesiboni yauma,minda ya mpesa ya ku Sibina yaguga.Atsogoleri a mitundu ina anapondapondaminda ya mpesa wabwino,imene nthambi zake zinakafika ku Yazeri,mpaka kutambalalira ku chipululu.Mizu yake inakafikampaka ku tsidya la nyanja.9Kotero Ine ndikulira, monga mmene akulirira anthu a ku Yazeri,chifukwa cha minda ya mpesa ya ku Sibima.Inu anthu a ku Hesiboni, inu anthu a ku Eleali,ndikukunyowetsani ndi misozi!Mwalephera kupeza zokolola,chifukwa cha nkhondo imene inawononga zokolola zonse.10Chimwemwe ndi chisangalalo zalekeka ku minda yanu ya zipatso;palibe amene akuyimba kapena kufuwula mʼminda ya mpesa;palibe amene akupsinya vinyo ku malo opsinyira mphesa,pakuti ndathetsa kufuwula.11Chifukwa chake moyo wanga ukulira ngati pangwe kulirira Mowabu,mtima wanga ukubuwula chifukwa cha Kiri Hareseti.12Ngakhale anthu a ku Mowabuapite ku malo awo achipembedzokoma amangodzitopetsa ndi kutaya nthawi chabechifukwa sizidzatheka.13Awa ndi mawu amene Yehova wayankhula kale zokhudza Mowabu.14Koma tsopano Yehova akuti, “Zisanathe zaka zitatu, potsata mʼmene munthu waganyu amawerengera, ulemerero wa Mowabu udzakhala utatheratu ndipo anthu ake ambiri adzakhala atawonongeka, ndipo opulumuka ake adzakhala ochepa ndi ofowoka.”