YESAYA10nya_bib
1Tsoka kwa anthu amene amapanga malamulo opanda chilungamo,kwa iwo amene amalemba zongovutitsa anzawo,2kuwalanda anthu osauka ufulu wawondi kumana chilungamo osautsidwa pakati pa anthu anga,amalanda zinthu za akazi amasiyendi kubera ana amasiye.3Kodi mudzatani pa tsiku la chilango,pofika chiwonongeko chochokera kutali?Kodi mudzathawira kwa yani kuti akuthandizeni?Nanga chuma chanu mudzachisiya kuti?4Kudzatsala nʼkungozolika mwamanyazi pakati pa anthu ogwidwakapena kufa pamodzi ndi ophedwa.Komabe pa zonsezi mkwiyo wake sunawachokere,mkono wake uli chitambasulire.