GENESIS10nya_bib
Mndandanda wa Mitundu ya Anthu
1Nayi mbiri ya ana a Nowa, Semu, Hamu ndi Yafeti. Ana atatuwa anabereka ana awo chitatha chigumula.Banja la Yafeti
2Ana aamuna a Yafeti anali: Gomeri, Magogi, Madai, Yavani, Tubala, Mesaki ndi Tirasi.3Ana aamuna a Gomeri anali: Asikenazi, Rifati ndi Togarima.4Ana aamuna a Yavani anali: Elisa, Tarisisi, Kitimu ndi Rodanimu.5(Amenewa ndiwo makolo a anthu okhala mʼmphepete mwa nyanja. Awa ndi ana a Yafeti monga mwa mafuko a mu mitundu yawo, uliwonse ndi chiyankhulo chake).Banja la Hamu
6Ana aamuna a Hamu anali: Kusi, Miziraimu, Puti ndi Kanaani.7Ana aamuna a Kusi anali: Seba, Havila, Sabita, Raama ndi Sabiteka. Ana aamuna a Raama anali: Seba ndi Dedani.8Kusi anabereka Nimurodi amene anali wankhondo wamphamvu kwambiri pa dziko lapansi.9Iye anali mlenje wamphamvu kwambiri pamaso pa Yehova; nʼchifukwa chake anthu ali ndi chisudzo, chakuti, “Ndiwe mlenje wamphamvu kwambiri pamaso pa Yehova monga Nimurodi.”10Malo oyambirira a ufumu wake anali Babeli, Ereki, Akadi ndi Kaline. Malo onsewa anali mʼdziko la Sinara.11Atachoka mʼdziko limeneli anapita ku Asiriya kumene anakamanga Ninive, Rehoboti-Iri, Kala,12ndi Reseni, mzinda waukulu umene uli pakati pa Ninive ndi Kala.13Igupto ndiye kholo la Aludi, Aanami, Alehabu, Anafutu,14Apaturusi, Akasilu ndi Akafitori (kumene kunachokera Afilisti).15Kanaani anabereka mwana wake wachisamba, Sidoni, ndipo anaberekanso Ahiti;16Ayebusi, Aamori, Agirigasi;17Ahivi, Aariki, Asini,18Aaravadi, Azemari ndi Ahamati.Pambuyo pake, mafuko a Akanaani anafalikira ponseponse,19mpaka ku malire a Kanaani. Malirewo anachokera ku Sidoni kulowa cha ku Gerari mpaka ku Gaza, ndi kulowa ku Sodomu, Gomora, Adima ndi Zeboimu mpaka ku Lasa.20Amenewa ndiwo ana aamuna a Hamu monga mwa mafuko ndi ziyankhulo zawo, mʼmadera omwe amakhala ndi mitundu yawo.