EZEKIELI19nya_bib

Nyimbo ya Maliro a Akalonga a Israeli

1“Imba nyimbo ya madandawulo, kuyimbira akalonga a ku Israeli.2Uzinena kuti,“ ‘Amayi ako anali ndani?Anali ngati mkango waukazi!Iwo unabwatama pakati pa mikango yayimuna;unkalera ana ake pakati pa misona.3Unalera mmodzi mwa ana ake,ndipo mwanayo anasanduka mkango wamphamvu.Unaphunzira kugwira nyama,ndipo unayamba kudya anthu.4Anthu amitundu anamva za mkangowo,ndipo tsiku lina unagwa mʼmbuna mwawo.Iwo anawukoka ndi ngowekupita nawo ku dziko la Igupto.
5“ ‘Amayi aja ataona kuti mwana ankamukhulupirira uja wagwidwa ndi kuti chiyembekezo chake chapita padera,amayiwo anatenganso mwana winanamusandutsa mkango wamphamvu.6Unkayendayenda pakati pa mikango inzake,pakuti tsopano unali mkango wamphamvu.Unaphunzira kugwira nyamandipo unayamba kudya anthu.7Unagwetsa malinga awo,ndikuwononga mizinda yawo.Onse a mʼdzikomoanachita mantha chifukwa cha kubangula kwake.8Pamenepo mitundu ya anthu, makamaka ochokera madera ozungulira,inabwera kudzalimbana nawo.Anawutchera ukonde wawo,ndipo tsiku lina unagwera mʼmbuna mwawo.9Anawukoka ndi ngowe nawuponya mʼchitatanga.Anabwera nawo kwa mfumu ya ku Babulonindipo mfumuyo inawuponya mʼndendendi cholinga choti liwu lake lisamamvekensoku mapiri a Israeli.
10“ ‘Amayi ako anali ngati mpesa mʼmunda wamphesawodzalidwa mʼmbali mwa madzi.Unabereka bwino ndipo unali ndi nthambi zambirichifukwa cha kuchuluka kwa madzi.11Nthambi zake zinali zolimba,zoyenera kupangira ndodo yaufumu.Unatalika nusomphoka pakati pazomera zina.Unkaoneka bwino chifukwa cha kutalika kwake,ndi nthambi zake zambiri.12Koma unazulidwa mwaukalindipo unagwetsedwa pansi.Unawuma ndi mphepo ya kummawa,zipatso zake zinayoyoka;nthambi zake zolimba zinafotandipo moto unapsereza mtengo wonse.13Ndipo tsopano anawuwokeranso ku chipululu,dziko lowuma ndi lopanda madzi.14Moto unatulukanso mu mtengomondi kupsereza nthambi ndi zipatso zake.Palibe nthambi yolimba inatsala pa mtengowoyoyenera kupangira ndodo yaufumu.Imeneyi ndi nyimbo yachisoni ndipo yasanduka nyimbo ya pa maliro.’ ”