DEUTERONOMO32nya_bib
1Mverani, inu mayiko a mmwamba ndipo ine ndidzayankhula;imva, iwe dziko lapansi, mawu a pakamwa panga.2Chiphunzitso changa chigwe ngati mvulandipo mawu anga atsike ngati mame,ngati mvumbi pa udzu watsopano,ngati mvula yochuluka pa zomera zanthete.3Ndidzalalikira dzina la Yehova.Aa, tamandani ukulu wa Mulungu wathu!4Iye ndi Thanthwe, ntchito zake ndi zangwiro,njira zake zonse ndi zolungama.Mulungu wokhulupirika amene salakwitsa,Iye ndiye wolungama ndi wosalakwa.5Koma iwo achita mosakhulupirika pamaso pake,iwo si ana akenso,koma iwo ndi mʼbado wachinyengo ndi wokhotakhota.6Kodi mukumubwezera Yehova chotere,inu anthu opusa ndi opanda nzeru?Kodi Iye si Atate anu, Mlengi wanu,amene anakupangani ndi kukuwumbani?7Kumbukirani masiku amakedzana;ganizirani za mibado yakalekale.Funsa abambo ako ndipo adzakuwuza,akuluakulu ako, ndipo adzakufotokozera.8Pamene Wammwambamwamba anapereka mayiko kwa anthu a mitundu ina kukhala cholowa chawo,pamene analekanitsa anthu onse,anayikira malire anthu onsemolingana ndi chiwerengero cha ana a Israeli.9Pakuti gawo la Yehova ndi anthu ake,Yakobo ndiye cholowa chake.10Anamupeza mʼchipululu,ku malo owuma ndi kopanda kanthu.Anamuteteza ndi kumusamalira;anamutchinjiriza ngati mwanadiso wake,11ngati chiwombankhanga chimene chimasasula chisa chakenʼkumazungulira pamwamba pa ana ake,chimene chimatambalalitsa mapiko ake kuti chigwire anawondi kuwanyamula pa mapiko ake otambalalawo.12Yehova yekha ndiye anamutsogolera;popanda thandizo la mulungu wachilendo.13Anamuyendetsa pamwamba pa mapiri a mʼdzikondi kumudyetsa zipatso za mʼminda.Anamudyetsa uchi wofula pa thanthwe,ndiponso mafuta ochokera mʼnthaka ya miyala,14pamodzi ndi chambiko ndi mkaka wochokera ku ngʼombe ndi nkhosa,ndiponso ana ankhosa onenepa ndi mbuzi,pamodzinso ndi nkhosa zazimuna zabwino za ku Basanindiponso tirigu wabwino kwambiri.Munamwa vinyo wa thovu lofiira.15Yesuruni ananenepa ndi kuyamba kuwukira;atakhuta, ananenepa ndi kukula thupi.Anasiya Mulungu amene anamulengandipo anakana Thanthwe ndi Mpulumutsi wake.16Anamuchititsa nsanje ndi milungu yawo yachilendondiponso anamukwiyitsa ndi mafano awo onyansa.17Anapereka nsembe kwa ziwanda zimene si Mulungu,milungu imene sankayidziwa nʼkale lomwe,milungu yongobwera kumene,milungu imene makolo anu sankayiopa.18Inu munasiya Thanthwe limene linakulerani;munayiwala Mulungu amene anakubalani.19Yehova anaona zimenezi ndipo anawakanachifukwa ana ake aamuna ndi aakazi anamukwiyitsa.20Iye anati, “Ndidzawabisira nkhope yanga,ndi kuona kuti mathero awo adzakhala otani;pakuti ndi mʼbado wopotoka,ana amene ndi osakhulupirika.21Anandichititsa kukhala wansanje pamene ankapembedza chimene si mulungundi kundikwiyitsa chifukwa cha mafano awo achabechabe.Ine ndidzawachititsa kuti achite nsanje ndi mtundu wina wopandapake;ndidzawakwiyitsa ndi mtundu wina wachabechabe.22Pakuti mkwiyo wanga wayaka ngati moto,umene umayaka mpaka ku dziko la anthu akufa.Motowo udzanyeketsa dziko lapansi ndi zokolola zakendipo udzapsereza maziko a mapiri.23“Ndidzawawunjikira masautsondipo mivi yanga yonse idzathera pa iwo.24Ndidzawatumizira njala yoopsa,malungo woopsa ndi nthenda zofa nazo;ndidzawatumizira zirombo zakuthengo zowavuta,ululu wa njoka ya mʼphiri imene imakwawa pa fumbi.25Mʼmisewu lupanga lidzawasandutsa kukhala wopanda ana;mantha adzalamulira nyumba zawo.Anyamata ndi atsikana adzafa,ngakhalenso makanda ndi okalamba.26Ine ndinanena kuti ndidzawamwazandi kuwafafaniza kuti anthu asawakumbukirenso,27koma sindinafune kuti adani anga adzandinyoze,mwina adani anga sadzandimvetsetsandipo adzanena kuti, ‘Tagonjetsa anthuwa ndife;Yehova sanachite zonsezi.’ ”28Iwo ndi mtundu wopanda maganizo,iwo alibe nzeru nʼpangʼono pomwe.29Ngati iwo akanakhala anzeru akanamvetsetsa izindi kuzindikira kuti mathero awo adzakhala otani!30Kodi munthu mmodzi akanathamangitsa bwanji anthu 1,000kapena anthu awiri kuthamangitsa anthu 10,000, kuti awagonjetse,Thanthwe lawo likanapanda kuwagulitsa,Yehova akanapanda kuwataya?31Pakuti thanthwe lawo silofanana ndi Thanthwe lathu,ngakhale adani athu amavomereza zimenezi.32Mpesa wawo umachokera ku mpesa wa ku Sodomundiponso ku minda ya ku Gomora.Mphesa zawo zili ndi ululu wakuphandipo maphava ake ndi owawa.33Vinyo wawo ndi wa ululu wa njoka,ululu woopsa wa mphiri.34“Kodi zimenezi sindinazisungendi kuzitsekera mʼkatikati mwa chuma changa?35Kubwezera chilango nʼkwanga; ndidzawalanga ndine.Pa nthawi yake phazi lawo lidzaterera;tsiku lawo la masautso layandikirandipo chiwonongeko chawo chikubwera pa iwo mofulumira.”36Yehova adzaweruza anthu akendipo adzachitira atumiki ake chifundopamene adzaona kuti mphamvu zawo zathandipo kuti palibe amene watsala, kapolo kapena mfulu.37Iye adzanena kuti, “Nanga ili kuti milungu yawo,thanthwe limene ankabisalamo,38milungu imene inkadya mafuta a nsembe zawondi kumwa vinyo wa chopereka chawo cha chakumwa?”Iwuzeni ibwere kuti idzakuthandizeni!Ibwere kuti idzakutetezenitu!39“Onani tsopano kuti Ine ndine Iyeyo!Palibe mulungu wina koma Ine ndekha.Ine ndimapha ndiponso kupereka moyo,ndavulaza ndipo ndidzachiritsa,ndipo palibe angathe kupulumutsa munthu mʼmanja mwanga.40Ndikweza dzanja langa kumwamba ndi kulumbira kuti,‘Pali Ine wamoyo wamuyaya,41pamene ndidzanola lupanga langa lonyezimirandipo dzanja liligwira pakubweretsa chiweruzo,ndidzabwezera chilango adani angandi kulanga onse odana nane.42Mivi yanga idzakhuta magazi awopamene lupanga langa lidzawononga mnofu:magazi a anthu ophedwa ndi ogwidwa ukapolo,mitu ya atsogoleri a adani.’ ”43Kondwerani, inu mitundu yonse ya anthu pamodzi ndi anthu ake,pakuti Iye adzabwezera chilango anthu amene anapha atumiki ake;adzabwezera chilango adani akendipo adzakhululukira dziko lake ndi la anthu ake.44Mose anabwera ndi Yoswa mwana wa Nuni ndipo anayankhula mawu onsewa mʼnyimbo anthu akumva.45Mose atatsiriza kunena mawu onsewa pamtima kwa Aisraeli,46iye anawawuza kuti, “Muwasunge bwino mu mtima mwanu, mawu onse amene lero lino ndikukuwuzani kuti mudzawuze ana anu, kuti adzamvere mosamalitsa mawu onse a malamulo amenewa.47Mawuwa sikuti ndi mawu achabe kwa inu. Mawuwa ndi moyo wanu. Mukawamvera mudzakhala ndi moyo wautali mʼdziko limene mukukalitenga kukhala lanu mukawoloka Yorodani.”