AMOSI3nya_bib

Mboni Zotsutsa Israeli

1Inu Aisraeli, imvani mawu awa amene Yehova wayankhula kutsutsana nanu, kutsutsana ndi banja lonse limene analitulutsa mu Igupto:2“Inu nokha ndi amene ndinakusankhanipakati pa mabanja onse a dziko lapansi;nʼchifukwa chake ndidzakulanganichifukwa cha machimo anu onse.”
3Kodi anthu awiri nʼkuyendera limodziasanapangane?4Kodi mkango umabangula mʼnkhalangousanagwire nyama?Kodi msona wamkango umalira mʼphanga mwakepamene sunagwire kanthu?5Kodi mbalame nʼkutera pa msamphapamene palibe nyambo yake?Kodi msampha umafwamphukausanakole kanthu?6Kodi pamene lipenga la nkhondo lalira mu mzinda,anthu sanjenjemera?Pamene tsoka lafika mu mzinda,kodi si Yehova amene wachititsa zimenezo?
7Zoonadi Ambuye Yehova sachita kanthuasanawulule zimene akufuna kuchitakwa atumiki ake, aneneri.
8Mkango wabangula,ndani amene sachita mantha?Ambuye Yehova wayankhula,ndani amene sanganenere?
9Lengezani zimenezi ku nyumba zaufumu za ku Asidodindiponso ku nyumba zaufumu za ku Igupto:“Sonkhanani ku mapiri a ku Samariya;onani chisokonezo pakati pakendiponso kuponderezana pakati pa anthu ake.”
10“Iwo sadziwa kuchita zolungama,ndipo amadzaza malo awo otetezedwa ndi zinthu zolanda ku nkhondo ndi zakuba,” akutero Yehova.11Nʼchifukwa chake Ambuye Yehova akunena izi:“Mdani adzalizungulira dzikoli;iye adzagwetsa malinga ako,ndi kufunkha nyumba zako zaufumu.”12Yehova akuti,“Monga mʼbusa amalanditsa mʼkamwa mwa mkangomiyendo iwiri yokha kapena msonga yokha ya khutu,moteronso ndimo mmene adzapulumukire Aisraeliamene amakhala mu Samariyapa msonga za mabedi awo,ndi ku Damasiko pa akakhutagona awo.”13“Imvani izi ndipo mupereke umboni wotsutsa nyumba ya Yakobo,” akutero Ambuye, Yehova Mulungu Wamphamvuzonse.14“Pa tsiku limene ndidzalange Israeli chifukwa cha machimo ake,ndidzagumula maguwa ansembe a ku Beteli;nyanga za guwa zidzathyokandipo zidzagwa pansi.15Ndidzagwetsa nyumba ya pa nthawi yozizirapamodzi ndi nyumba ya pa nthawi yotentha;nyumba zokongoletsedwa ndi minyanga ya njovu zidzawonongedwandipo nyumba zikuluzikulu zidzaphwasulidwa,”akutero Yehova.