1 MAFUMU4nya_bib
Nduna za Solomoni ndi Abwanamkubwa
1Ndipo Mfumu Solomoni inakhala mfumu ya Aisraeli onse.2Nduna zake zikuluzikulu zinali izi:Azariya mwana wa Zadoki anali wansembe;3Elihorefe ndi Ahiya, ana a Sisa, anali alembi; Yehosafati mwana wa Ahiludi, anali mlembi wa zochitika;4Benaya mwana wa Yehoyada, anali mtsogoleri wa ankhondo; Zadoki ndi Abiatara, anali ansembe;5Azariya mwana wa Natani, anali woyangʼanira nduna za mʼzigawo; Zabudi mwana wa Natani, anali wansembe ndi bwenzi la mfumu;6Ahisara, anali mkulu woyangʼanira nyumba ya mfumu; Adoniramu mwana wa Abida, anali mkulu woyangʼanira ntchito za thangata.7Solomoni analinso ndi abwanamkubwa khumi ndi awiri amene ankayangʼanira zigawo zonse za dziko la Israeli. Iwo ankapereka chakudya kwa mfumu ndiponso ku banja laufumu. Bwanamkubwa aliyense ankapereka chakudya mwezi umodzi pa chaka.8Mayina awo ndi awa:
Beni-Huri, wa ku dziko la mapiri la Efereimu;9Beni-Dekeri, woyangʼanira mizinda ya Makazi, Saalibimu, Beti-Semesi ndi Eloni Beti-Hanani;10Beni-Hesedi, woyangʼanira mizinda ya Aruboti (Soko ndi dziko lonse la Heferi);11Beni-Abinadabu, woyangʼanira Nafoti Dori (iye anakwatira Tafati mwana wa Solomoni);12Baana mwana wa Ahiludi, anali woyangʼanira Taanaki ndi Megido, ndi ku Beti Sani konse, kufupi ndi ku Zaretani kumunsi kwa Yezireeli, kuyambira ku Beti-Seani mpaka ku Abeli-Mehola kukafika mpaka ku Yokineamu;13Beni-Geberi, anali woyangʼanira Ramoti Giliyadi (midzi ya Yairi inali ya mwana wa Manase ku Giliyadi, pamodzinso ndi chigawo cha Arigobu ku Basani ndiponso mizinda yake yayikulu makumi asanu ndi umodzi yokhala ndi malinga ndi mipiringidzo yamkuwa).14Ahinadabu mwana wa Ido, anali woyangʼanira Mahanaimu;15Ahimaazi anali woyangʼanira Nafutali (iyeyu anakwatira Basemati mwana wa Solomoni);16Baana mwana wa Husai, anali woyangʼanira Aseri ndi Bealoti;17Yehosafati mwana wa Paruwa, anali woyangʼanira Isakara;18Simei mwana wa Ela, anali woyangʼanira Benjamini;19Geberi mwana wa Uri, anali woyangʼanira Giliyadi (dziko la Sihoni mfumu ya Aamori ndi dziko la Ogi mfumu ya Basani). Iye ankayangʼanira chigawo chonsechi yekha.