1 MBIRI6nya_bib
Fuko la Levi
1Ana a Levi anali awa: Geresoni, Kohati ndi Merari.2Ana a Kohati anali awa: Amramu, Izihari, Hebroni ndi Uzieli.3Ana a Amramu anali awa: Aaroni, Mose ndi Miriamu. Ana a Aaroni anali awa: Nadabu, Abihu, Eliezara ndi Itamara4Eliezara anabereka Finehasi, Finehasi anabereka Abisuwa,5Abisuwa anabereka Buki, Buki anabereka Uzi.6Uzi anabereka Zerahiya, Zerahiya anabereka Merayoti,7Merayoti anabereka Amariya, Amariya anabereka Ahitubi.8Ahitubi anabereka Zadoki, Zadoki anabereka Ahimaazi.9Ahimaazi anabereka Azariya, Azariya anabereka Yohanani,10Yohanani anabereka Azariya (uyu ndi amene anatumikira monga wansembe mʼNyumba ya Mulungu imene Solomoni anamanga mu Yerusalemu),11Azariya anabereka Amariya, Amariya anabereka Ahitubi,12Ahitubi anabereka Zadoki, Zadoki anabereka Salumu,13Salumu anabereka Hilikiya, Hilikiya anabereka Azariya,14Azariya anabereka Seraya, ndipo Seraya anabereka Yehozadaki.15Yehozadaki anagwidwa ukapolo pamene Yehova analola Nebukadinezara kuti agwire ukapolo Yuda ndi Yerusalemu.16Ana a Levi anali awa: Geresomu, Kohati ndi Merari.17Mayina a ana a Geresomu ndi awa: Libini ndi Simei.18Ana a Kohati anali awa: Amramu, Izihari, Hebroni ndi Uzieli.19Ana a Merari anali awa: Mahili ndi Musi.Mayina a mabanja a fuko la Levi olembedwa potsata makolo awo ndi awa:20Ana a Geresomu ndi awa: Libini, Yehati, Zima,21Yowa, Ido, Zera ndi Yeaterai.22Zidzukulu za Kohati ndi izi: Aminadabu, Kora, Asiri,23Elikana, Ebiyasafu, Asiri,24Tahati, Urieli, Uziya ndi Sauli.25Zidzukulu za Elikana ndi izi: Amasai, Ahimoti,26Elikana, Zofai, Nahati,27Eliabu, Yerohamu, Elikana ndi Samueli.28Ana a Samueli ndi awa: Mwana wake woyamba anali Yoweli, wachiwiri anali Abiya.29Zidzukulu za Merari ndi izi: Mahili, Libini, Simei, Uza,30Simea, Hagiya ndi Asaya.