1 MBIRI26nya_bib
Alonda a pa Zipata
1Magulu a alonda a pa zipata:Kuchokera ku banja la Kora: Meselemiya mwana wa Kore, mmodzi mwa ana a Asafu.2Meselemiya anali ndi ana awa: woyamba Zekariya, wachiwiri Yediaeli, wachitatu Zebadiya, wachinayi Yatinieli,3wachisanu Elamu, wachisanu ndi chimodzi Yehohanani, ndipo wachisanu ndi chiwiri Elihunai.4Obedi-Edomu analinso ndi ana awa: woyamba Semaya, wachiwiri Yehozabadi, wachitatu Yowa, wachinayi Sakara, wachisanu Netaneli,5wachisanu ndi chimodzi Amieli, wachisanu ndi chiwiri Isakara ndipo wachisanu ndi chitatu Peuletayi. (Pakuti Mulungu anadalitsa Obedi-Edomu).6Mwana wake Semaya analinso ndi ana amene anali atsogoleri mʼbanja la abambo awo chifukwa anali anthu amphamvu.7Ana a Semaya anali: Otini, Refaeli, Obedi ndi Elizabadi; abale ake, Elihu ndi Semakiya, analinso anthu amphamvu.8Onsewa anali adzukulu a Obedi-Edomu. Iwo ndi ana awo ndiponso abale awo anali anthu aluso ndi amphamvu pogwira ntchito. Zidzukulu zonse za Obedi-Edomu zinalipo 62.9Meselemiya anali ndi ana ndi abale ake amene anali aluso ndipo onse analipo 18.10Hosa Mmerari anali ndi ana awa: woyamba anali Simiri (ngakhale kuti iye sanali woyamba kubadwa, abambo ake anamusankha kuti akhale mtsogoleri),11wachiwiri Hilikiya, wachitatu Tebaliya ndipo wachinayi Zekariya. Ana ndi abale onse a Hosa analipo 13.12Magulu amenewa a alonda a pa zipata, motsogozedwa ndi atsogoleri awo, anali ndi ntchito yotumikira mʼNyumba ya Yehova, monga momwe amachitira abale awo.13Iwo anachita maere mwa mabanja awo aangʼono ndi aakulu omwe kuti apeze mlonda pa chipata chilichonse.14Maere a chipata chakummwa anagwera Selemiya. Maere anachitikanso chifukwa cha mwana wake Zekariya, phungu wanzeru ndipo maere a chipata chakumpoto anagwera iye.15Maere a chipata chakummwera anagwera Obedi-Edomu, ndipo maere a nyumba yosungiramo katundu anagwera ana ake.16Maere a chipata chakumadzulo ndi chipata cha Saleketi ku msewu wa ku mtunda anagwera Supimu ndi Hosa. Mlonda ankayangʼanana ndi mlonda mnzake:17Mbali ya kummawa kunkakhala Alevi 6 pa tsiku, kumpoto anayi pa tsiku, kummwera anayi pa tsiku ndipo awiri ankakhala pa nyumba yosungiramo katundu.18Ndipo ku bwalo cha kumadzulo, anayi amakhala mu msewu ndi awiri pabwalo penipeni.19Awa anali magulu a alonda a pa zipata amene anali zidzukulu za Kora ndi Merari.