1 MBIRI16nya_bib
1Iwo anabwera nalo Bokosi la Mulungu ndipo analiyika pamalo pake mʼkati mwa tenti imene Davide anayimika ndipo iwo anapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano pamaso pa Mulungu.2Davide atatsiriza kupereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano, iye anadalitsa anthu mʼdzina la Yehova.3Kenaka anagawira Mwisraeli aliyense, wamwamuna ndi wamkazi, aliyense buledi mmodzi, nthuli yanyama ndiponso keke yamphesa zowuma.4Iye anasankha Alevi ena kuti azitumikira pamene panali Bokosi la Yehova, kuti azipemphera, azithokoza ndi kulemekeza Yehova Mulungu wa Israeli.5Mtsogoleri wawo anali Asafu, wachiwiri anali Zekariya, kenaka Yeiyeli, Semiramoti, Yehieli, Matitiya, Eliabu, Benaya, Obedi-Edomu ndi Yeiyeli. Iwo amayimba azeze ndi apangwe, Asafu amayimba ziwaya za malipenga,6ndipo ansembe Benaya ndi Yahazieli amawomba malipenga nthawi zonse pamaso pa Bokosi la Chipangano la Mulungu.